Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 19:5 - Buku Lopatulika

5 nati, Chifukwa cha ichi mwamuna adzasiya atate wake ndi amake, nadzaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 nati, Chifukwa cha ichi mwamuna adzasiya atate wake ndi amake, nadzaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ndipo kuti Iye yemweyo adati, ‘Nchifukwa chake mwamuna azisiya atate ake ndi amai ake, nakaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo aŵiriwo adzasanduka thupi limodzi.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ndipo anati, ‘Pa chifukwa ichi mwamuna adzasiya abambo ake ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.’

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 19:5
19 Mawu Ofanana  

Ndipo mtima wake unakhumba Dina mwana wake wamkazi wa Yakobo, ndipo anamkonda namwaliyo, nanena momkopa namwaliyo.


Ndipsinjika mtima chifukwa cha iwe, mbale wanga Yonatani; wandikomera kwambiri; chikondi chako, ndinadabwa nacho, chinaposa chikondi cha anthu aakazi.


a mitundu ija Yehova adanena ndi ana a Israele za iwo, kuti, Inu musakalowa kwa iwo, ndipo iwo asadzalowe kwa inu; zedi adzatembenuza mitima yanu kutsata milungu yao; amenewo Solomoni anawaumirira kuwakonda.


Tamvera, mwana wamkaziwe, taona, tatchera khutu lako; uiwalenso mtundu wako ndi nyumba ya atate wako;


Moyo wanga uumirira Inu. Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza.


Ndipo sanatero kodi wina womtsalira mzimu? Ndipo winayo anatero bwanji? Anatero pofuna mbeu ya Mulungu. Koma sungani mzimu wanu; ndipo asamchitire monyenga mkazi wa ubwana wake ndi mmodzi yense.


Chotero kuti salinso awiri koma thupi limodzi. Chifukwa chake ichi chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.


Chikondano chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choipa; gwirizana nacho chabwino.


Kapena simudziwa kuti iye wophatikidwa ndi mkazi wachiwerewere ali thupi limodzi? Pakuti awiriwo, ati, adzakhala thupi limodzi.


Koma chifukwa cha madama munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.


Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mwamuna ndiye; koma momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi la iye yekha, koma mkazi ndiye.


Chifukwa cha ichi munthu azisiya atate ndi amai, nadzaphatikizana ndi mkazi wake; ndipo iwo awiri adzakhala thupi limodzi.


Muziopa Yehova Mulungu wanu; mumtumikire Iyeyo; mummamatire Iye, ndi kulumbira pa dzina lake.


Pakuti mukasunga chisungire malamulo awa onse amene ndikuuzani kuwachita; kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake zonse, ndi kummamatira;


Koma inu amene munamamatira Yehova Mulungu wanu muli ndi moyo nonsenu lero lomwe.


Ndipo kunali, pakutsiriza iye kulankhula ndi Saulo, mtima wa Yonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Yonatani anamkonda iye monga moyo wa iye yekha.


Davide anatenganso Ahinowamu wa ku Yezireele, ndipo onse awiri anakhala akazi ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa