Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 19:10 - Buku Lopatulika

10 Ophunzira ananena kwa Iye, Ngati mlandu wa munthu ndi mkazi wake uli wotere, sikuli kwabwino kukwatira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ophunzira ananena kwa Iye, Ngati mlandu wa munthu ndi mkazi wake uli wotere, sikuli kwabwino kukwatira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Ophunzira ake adamuuza kuti, “Ndiyetu ngati zili choncho pakati pa mwamuna ndi mkazi wake, ndi bwino tsono kusakwatira.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ophunzira ake anati kwa Iye, “Ngati umu ndi mmene zilili pa mwamuna ndi mkazi, kuli bwino kusakwatira.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 19:10
15 Mawu Ofanana  

Yehova Mulungu ndipo anati, Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzampangira womthangatira iye.


Wopeza mkazi apeza chinthu chabwino; Yehova amkomera mtima.


Kukhala m'chipululu kufunika kuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wong'ung'udza.


Kukhala pangodya ya tsindwi kufunika kuposa kukhala m'nyumba ndi mkazi wolongolola.


Koma Iye anati kwa iwo, Onse sangathe kulandira chonena ichi, koma kwa iwo omwe chapatsidwa.


Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo: ndipo iye amene akwatira wochotsedwayo, achita chigololo.


Koma ndinena kwa osakwatira, ndi kwa akazi amasiye, kuti kuli bwino kwa iwo ngati akhala monganso ine.


a kuletsa ukwati, osiyitsa zakudya zakuti, zimene Mulungu anazilenga kuti achikhulupiriro ndi ozindikira choonadi azilandire ndi chiyamiko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa