Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 18:31 - Buku Lopatulika

31 Chifukwa chake m'mene akapolo anzake anaona zochitidwazo, anagwidwa chisoni chachikulu, nadza, nalongosolera mbuye wao zonse zimene zinachitidwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Chifukwa chake m'mene akapolo anzake anaona zochitidwazo, anagwidwa chisoni chachikulu, nadza, nalongosolera mbuye wao zonse zimene zinachitidwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 “Antchito anzake ena ataona zimenezi, adamva chisoni kwambiri. Adapita kukafotokozera mbuye wao zonsezo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Pamene antchito ena anaona zomwe zinachitikazo, anamva chisoni kwambiri ndipo anapita nakawuza bwana wawo zonse zimene zinachitika.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 18:31
16 Mawu Ofanana  

Mibadwo ya Yakobo ndi iyi; Yosefe anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri analinkudyetsa zoweta pamodzi ndi abale ake; ndipo anali mnyamata pamodzi ndi ana a Biliha, ndi ana aamuna a Zilipa, akazi a atate wake; ndipo Yosefe anamfotokozera atate wake mbiri yao yoipa.


Maso anga atsitsa mitsinje ya madzi, popeza sasamalira chilamulo chanu.


Ndinapenya ochita monyenga, ndipo ndinanyansidwa nao; popeza sasamalira mau anu.


Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!


Ndipo mfumuyo anagwidwa ndi chisoni; koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo anali naye pachakudya, analamulira upatsidwe;


Koma kapolo uyu, potuluka anapeza wina wa akapolo anzake yemwe anamkongola iye marupiya atheka makumi khumi, namgwira, namkanyanga pakhosi, nati, Bwezera chija unachikongola.


Ndipo iye sanafune; koma anamuka, namponya iye m'nyumba yandende, kufikira abwezere ngongole.


Pomwepo mbuye wake anamuitana iye, nanena naye, Kapolo iwe woipa, ndinakukhululukira iwe mangawa onse aja momwe muja unandipempha ine;


Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake.


Ndipo kapoloyo pakubwera anauza mbuye wake zinthu izi. Pamenepo mwini nyumba anakwiya, nati kwa kapolo wake, Tuluka msanga, pita kumakwalala ndi kunjira za mzinda, nubwere nao muno aumphawi ndi opunduka ndi akhungu ndi otsimphina.


Ndipo m'mene anayandikira, anaona mzindawo naulirira,


Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira.


Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tinakhala ofooka. Koma m'mene wina alimbika mtimamo (ndinena mopanda nzeru) momwemo ndilimbika mtima inenso.


Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.


Kumbukirani am'nsinga, monga am'nsinga anzao; ochitidwa zoipa, monga ngati inunso adatero nanu m'thupi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa