Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 17:12 - Buku Lopatulika

12 koma ndinena kwa inu, kuti Eliya anadza kale, ndipo iwo sanamdziwe iye, koma anamchitira zonse zimene anazifuna iwo. Ndipo chonchonso Mwana wa Munthu adzazunzidwa ndi iwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 koma ndinena kwa inu, kuti Eliya anadza kale, ndipo iwo sanamdziwe iye, koma anamchitira zonse zimene anazifuna iwo. Ndipo chonchonso Mwana wa Munthu adzazunzidwa ndi iwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Koma ndikunenetsa kuti Eliya adabwera kale, ndipo anthu sadamzindikire, koma adamchita zonse zimene iwo ankafuna. Chonchonso Mwana wa Munthu adzazunzidwa ndi anthuwo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Koma Ine ndikuwuzani inu kuti Eliya anabwera kale koma iwo sanamuzindikire ndipo anachita naye chilichonse chimene anafuna. Momwemonso iwo adzazunza Mwana wa Munthu.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 17:12
25 Mawu Ofanana  

Koma Yohane, pakumva m'nyumba yandende ntchito za Khristu, anatumiza ophunzira ake mau,


Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa.


Ndipo Iye anayankha, nati, Eliya akudzatu, nadzabwezera zinthu zonse;


Pomwepo ophunzira anazindikira kuti analankhula nao za Yohane Mbatizi.


Ndipo m'mene anali kutsotsa mu Galileya, Yesu ananena nao, Mwana wa Munthu adzaperekedwa m'manja a anthu;


Ndipo pamene anali kutsika paphiri, Yesu anawalamula iwo kuti, Musakauze munthu choonekacho, kufikira Mwana wa Munthu adadzauka kwa akufa.


Popeza Yohane anadza kwa inu m'njira ya chilungamo, ndipo simunamvere iye; koma amisonkho ndi akazi achiwerewere anammvera iye; ndipo inu, m'mene munachiona, simunalape pambuyo pake, kuti mumvere iye.


Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m'mlengalenga zisa zao, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu wake.


Pakuti Yohane Mbatizi wafika wosadya mkate ndi wosamwa vinyo; ndipo munena, Ali ndi chiwanda.


Anadza kwa zake za Iye yekha, ndipo ake a mwini yekha sanamlandire Iye.


ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwampachika ndi kumupha ndi manja a anthu osaweruzika;


zindikirani inu nonse, ndi anthu onse a Israele, kuti m'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, amene inu munampachika pamtanda, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, mwa Iyeyu munthuyu aimirirapo pamaso panu, wamoyo.


Ndiye yani wa aneneri makolo anu sanamzunze? Ndipo anawapha iwo amene anaonetseratu za kudza kwake kwa Wolungamayo; wa Iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa