Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 15:5 - Buku Lopatulika

5 Koma inu munena, Aliyense amene anena kwa atate wake kapena kwa amake, Icho ukanathandizidwa nacho, nchoperekedwa kwa Mulungu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Koma inu munena, Amene aliyense anena kwa atate wake kapena kwa amake, Icho ukanathandizidwa nacho, nchoperekedwa kwa Mulungu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Koma inu mumati, ‘Munthu akauza atate ake kapena amai ake kuti, “Zimene ndikadakuthandiza nazoni, ndazipereka kwa Mulungu,” ameneyo sasoŵanso kulemekeza atate ake.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, ‘Thandizo lililonse mukalirandira kuchokera kwa ine ndi mphatso yoperekedwa kwa Mulungu,’

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 15:5
9 Mawu Ofanana  

Kunena mwansontho, Ichi nchopatulika, kuli msampha kwa munthu, ndi kusinkhasinkha pambuyo pake atawinda.


Pakuti Mulungu anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo, Wakunenera atate wake ndi amake zoipa, afe ndithu.


iyeyo sadzalemekeza atate wake. Ndipo inu mupeputsa mau a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu.


Koma Petro ndi Yohane anayankha nati kwa iwo, Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu;


Ndipo anayankha Petro ndi atumwi, nati, Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa