Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 14:3 - Buku Lopatulika

3 Pakuti Herode adamgwira Yohane, nammanga, namuika m'nyumba yandende chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa mbale wake Filipo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pakuti Herode adamgwira Yohane, nammanga, namuika m'nyumba yandende chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa mbale wake Filipo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Pajatu Herode kale adaatuma asilikali ake kuti akagwire Yohane, akammange ndi kumponya m'ndende. Adaachita zimenezi chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo, mbale wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Pakuti Herode anamugwira Yohane ndi kumumanga ndipo anamuyika mʼndende chifukwa cha Herodia mkazi wa mʼbale wake Filipo.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 14:3
18 Mawu Ofanana  

Koma Yohane, pakumva m'nyumba yandende ntchito za Khristu, anatumiza ophunzira ake mau,


Koma pakufika tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiasi anavina pakati pao, namkondweretsa Herode.


Ndipo pamene Yesu anamva kuti anampereka Yohane, anamuka kulowa ku Galileya;


Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lake lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo chifukwa chake mphamvu izi zichitachita mwa Iye.


Pakuti Herode, mwini yekha, adatuma anthu namgwira Yohane, nammanga m'nyumba yandende, chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo mbale wake; chifukwa adamkwatira iye.


Ndipo Herodiasi anamuda, nafuna kumupha; koma sanakhoze;


ndipo pamene mwana wamkazi wa Herodiasi analowa yekha navina, anakondwetsa Herode ndi iwo akukhala naye pachakudya; ndipo mfumuyo inati kwa buthulo, Tapempha kwa ine chilichonse uchifuna, ndidzakupatsa iwe.


Ndipo Iye anawalamula, nanena, Yang'anirani, penyani kuti mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi, ndi chotupitsa mkate cha Herode.


Ndipo anakhalako nthawi yomweyo, anthu ena amene anamuuza Iye za Agalileya, amene Pilato anasakaniza mwazi wao ndi nsembe zao.


Nthawi yomweyo anadzapo Afarisi ena, nanena kwa Iye, Tulukani, chokani kuno; chifukwa Herode afuna kupha Inu.


Ndipo Herode ndi asilikali ake anampeputsa Iye, namnyoza, namveka Iye chofunda chonyezimira, nambwezera kwa Pilato.


Ndipo m'mene anadziwa kuti ali wa mu ulamuliro wake wa Herode, anamtumiza Iye kwa Herode, amene anali iye mwini ku Yerusalemu masiku awa.


Ndipo pa chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberio Kaisara, pokhala Pontio Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode chiwanga cha Galileya, ndi Filipo mbale wake chiwanga cha dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lisaniasi chiwanga cha Abilene;


ndi Yohana, mkazi wake wa Kuza kapitao wa Herode, ndi Suzana, ndi ena ambiri, amene anawatumikira ndi chuma chao.


Koma nyengo imeneyo Herode mfumu anathira manja ena a mu Mpingo kuwachitira zoipa.


Pakuti zoonadi anasonkhanidwa m'mzinda muno Herode, ndi Pontio Pilato yemwe pamodzi ndi amitundu ndi anthu a Israele kumchitira choipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene munamdzoza;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa