Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 13:55 - Buku Lopatulika

55 Kodi uyu si mwana wa mmisiri wa mitengo? Kodi dzina lake la amake si Maria? Ndi abale ake si Yakobo ndi Yosefe ndi Simoni ndi Yuda?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

55 Kodi uyu si mwana wa mmisiri wa mitengo? Kodi dzina lake la amake si Maria? Ndi abale ake si Yakobo ndi Yosefe ndi Simoni ndi Yuda?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

55 Kodi ameneyu si mwana wa mmisiri wa matabwa uja? Kodi suja mai wake ndi Maria? Ndipo abale ake si Yakobe, Yosefe, Simoni ndi Yuda?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

55 Kodi si mwana wa wopala matabwa? Kodi dzina la amayi ake si Mariya ndipo kodi abale ake si Yakobo, Yosefe, Simoni ndi Yudasi?

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 13:55
23 Mawu Ofanana  

Koma ine ndine nyongolotsi, si munthu ai, chotonza cha anthu, ndi wonyozedwa ndi anthu.


Atero Yehova, Mombolo wa Israele, ndi Woyera wake, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyasidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira chifukwa cha Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israele, amene anakusankha Iwe.


mwa iwo amene munali Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi wa Yosefe, ndi amake wa ana a Zebedeo.


Ndipo analinso kumeneko akazi akuyang'anira kutali; mwa iwo anali Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo wamng'ono ndi wa Yosefe, ndi Salome;


Ndipo Maria wa Magadala ndi Maria amake wa Yosefe anapenya pomwe anaikidwapo.


Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Maria, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yudasi, ndi Simoni? Ndipo alongo ake sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye.


kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, dzina lake Yosefe, wa fuko la Davide; ndipo dzina lake la namwaliyo ndilo Maria.


Koma panali Maria wa Magadala, ndi Yohana, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi akazi ena pamodzi nao amene ananena izi kwa atumwiwo.


Ndipo Yesuyo, pamene anayamba ntchito yake, anali monga wa zaka makumi atatu, ndiye (monga anthu adamuyesa) mwana wa Yosefe, mwana wa Eli,


Ndipo onse anamchitira Iye umboni nazizwa ndi mau a chisomo akutuluka m'kamwa mwake; nanena, Kodi uyu si mwana wa Yosefe?


Ndipo anamuuza Iye, kuti, Amai wanu ndi abale anu alinkuima kunja, nafuna kuona Inu.


Koma pamtanda wa Yesu anaimirira amake, ndi mbale wa amake, Maria, mkazi wa Kleopa, ndi Maria wa Magadala.


Ndipo iwo ananena, Si Yesu uyu, mwana wa Yosefe, atate wake ndi amai wake tiwadziwa? Anena bwanji tsopano, kuti, Ndinatsika Kumwamba?


Tidziwa ife kuti Mulungu analankhula ndi Mose; koma sitidziwa kumene achokera ameneyo.


Koma wina wa atumwi sindinamuone, koma Yakobo mbale wa Ambuye.


Yuda, kapolo wa Yesu Khristu, ndi mbale wa Yakobo, kwa iwo oitanidwa, okondedwa mwa Mulungu Atate, ndi osungidwa ndi Yesu Khristu:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa