Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 13:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo anyamata ake a mwini nyumbayo anadza, nati kwa iye, Mbuye, kodi simunafese mbeu zabwino m'munda mwanu? Nanga wachokera kuti namsongoleyo?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo anyamata ake a mwini nyumbayo anadza, nati kwa iye, Mbuye, kodi simunafesa mbeu zabwino m'munda mwanu? Nanga wachokera kuti namsongoleyo?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Antchito a mwinimunda uja adadzamufunsa kuti, ‘Bwana, kodi suja mudaafesa mbeu zabwino m'munda mwanu? Nanga bwanji mukuwonekanso namsongole?’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 “Antchito ake anabwera kwa iye ndi kuti, ‘Bwana, kodi simunafese mbewu zabwino mʼmunda mwanu? Nanga namsongole wachokera kuti?’

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 13:27
17 Mawu Ofanana  

koma m'mene anthu analinkugona, mdani wake anadza, nafesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo.


Koma pamene mmera unakula, nubala chipatso, pomwepo anaonekeranso namsongole.


Ndipo iye ananena kwa iwo, Munthu mdani wanga wachichita ichi. Ndipo anyamata anati kwa iye, Kodi mufuna tsopano kuti timuke, tikamsonkhanitse uyo pamodzi?


Pakuti Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu mwini banja, amene anatuluka mamawa kukalembera antchito a m'munda wake wampesa.


Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang'anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo.


Koma akadza Timoteo, penyani kuti akhale ndi inu wopanda mantha; pakuti agwira ntchito ya Ambuye, monganso ine;


Ndipo ochita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu,


koma m'zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu, m'kupirira kwambiri, m'zisautso, m'zikakamizo, m'zopsinja,


Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa