Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 13:15 - Buku Lopatulika

15 Chifukwa unalemera mtima wa anthu awa, ndipo m'makutu ao anamva mogontha, ndipo maso ao anatsinzina; kuti asaone konse ndi maso, asamve ndi makutu, asazindikire ndi mtima wao, asatembenuke, ndipo ndisawachiritse iwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Chifukwa unalemera mtima wa anthu awa, ndipo m'makutu ao anamva mogontha, ndipo maso ao anatsinzina; kuti asaone konse ndi maso, asamve ndi makutu, asazindikire ndi mtima wao, asatembenuke, ndipo ndisawachiritse iwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Ndithu anthu ameneŵa nzeru zao nzobuntha, adagonthetsa makutu ao, ndipo adapsinya maso ao, kuwopa kuti angamapenye ndi maso aowo, angamamve ndi makutu aowo, angamamvetse ndi nzeru zaozo, ndi kutembenuka mtima, Ineyo nkuŵachiritsa.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Pakuti mtima wa anthu awa ndi wokanika, mʼmakutu mwawo ndi mogontha, ndipo atsinzina kuti asaone kanthu. Mwina angapenye ndi maso awo, angamve ndi makutu awo, angamvetse ndi nzeru zawo ndi kutembenuka, Ineyo nʼkuwachiritsa.’

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 13:15
25 Mawu Ofanana  

Mtima wao unona ngati mafuta; koma ine ndikondwera nacho chilamulo chanu.


Wotsinzina ndiye aganizira zokhota; wosunama afikitsa zoipa.


Iye adya phulusa; mtima wodzinyenga wampambutsa, kuti iye sangapulumutse moyo wake, pena kunena, Kodi simuli kunama m'dzanja langa lamanja?


Ndaona njira zake, ndipo ndidzamchiritsa; ndidzamtsogoleranso, ndi kumbwezera iye ndi olira maliro ake zotonthoza mtima.


Nenepetsa mtima wa anthu awa, lemeretsa makutu ao, nutseke maso ao; angaone ndi maso ao, angamve ndi makutu ao, angazindikire ndi mtima wao, nakabwerenso, nachiritsidwe.


Mundichiritse ine, Yehova, ndipo ndidzachiritsidwa; mundipulumutse ine, ndipo ndidzapulumutsidwa; pakuti chilemekezo changa ndinu.


Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziwa?


Bwerani, ana inu obwerera, ndidzachiritsa mabwerero anu. Taonani, tadza kwa Inu; pakuti ndinu Yehova Mulungu wathu.


Taonani, ndidzautengera moyo ndi kuuchiritsa, ndi kuwachiritsa; ndipo ndidzawaululira iwo kuchuluka kwa mtendere ndi zoona.


Ndidzachiritsa kubwerera kwao, ndidzawakonda mwaufulu; pakuti mkwiyo wanga wamchokera.


Koma anakana kumvera, nakaniza phewa lao, natseka makutu ao, kuti asamve.


Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m'mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati anaang'ombe onenepa otuluka m'khola.


kuti kupenya apenye, koma asazindikire; ndipo kumva amve, koma asadziwitse; kuti pena angatembenuke, ndi kukhululukidwa.


nanena, Ukadazindikira tsiku ili, inde iwetu zinthu za mtendere! Koma tsopano zibisika pamaso pako.


pakuti mtima wa anthu awa watupatu, ndipo m'makutu mwao mmolema kumva, ndipo maso ao anawatseka; kuti angaone ndi maso, nangamve ndi makutu, nangazindikire ndi mtima, nangatembenuke, ndipo Ine ndingawachiritse.


Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera kunkhope ya Ambuye;


Koma anafuula ndi mau aakulu, natseka m'makutu mwao, namgumukira iye ndi mtima umodzi;


ndipo adzalubza dala pachoonadi, nadzapatukira kutsata nthano zachabe.


Za iye tili nao mau ambiri kuwanena, ndi otivuta powatanthauzira, popeza mwagontha m'makutu.


Pakati pa khwalala lake, ndi tsidya ili la mtsinje, ndi tsidya lake lija panali mtengo wa moyo wakubala zipatso khumi ndi ziwiri, ndi kupatsa zipatso zake mwezi ndi mwezi; ndipo masamba a mtengo ndiwo akuchiritsa nao amitundu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa