Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 11:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo panali, pamene Yesu anatha kuwafotokozera ophunzira ake khumi ndi awiri, Iye anachokera kumeneko kukaphunzitsa ndi kulalikira m'mizinda mwao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo panali, pamene Yesu anatha kuwafotokozera ophunzira ake khumi ndi awiri, Iye anachokera kumeneko kukaphunzitsa ndi kulalikira m'midzi mwao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Yesu atatsiriza kulangiza ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja, adachoka kumeneko nkumakaphunzitsa ndi kulalika m'mizinda yao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ndipo Yesu atamaliza kulangiza ophunzira ake khumi ndi awiri aja, anachoka kumeneko kupita kukaphunzitsa ndi kukalalikira ku mizinda ya ku Galileya.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 11:1
19 Mawu Ofanana  

ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.


Ndipo Yesu anayendayenda mu Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.


Ndipo panakhala pamene Yesu anatha mau amenewa, makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake:


Ndipo Yesu anayendayenda m'mizinda yonse ndi m'midzi, namaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumuwo, nachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.


Ndipo anatuluka nalalikira kuti anthu atembenuke mitima.


Koma iwo anapunda kunena kuti, Amautsa anthuwo, naphunzitsa mu Yudeya yense, kuyambira ku Galileya ndi kufikira kuno komwe.


Ndipo kunali, katapita kamphindi anayendayenda kumizinda ndi kumidzi, kulalikira ndi kuwauza Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndi pamodzi naye khumi ndi awiriwo,


Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'chikondi changa; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'chikondi chake.


Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulani inu.


kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba, atatha kulamula mwa Mzimu Woyera atumwi amene adawasankha;


za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.


Ndipo anatilamulira ife tilalikire kwa anthu, ndipo tichite umboni kuti Uyu ndiye amene aikidwa ndi Mulungu akhale woweruza amoyo ndi akufa.


Pakuti mudziwa malangizo amene tinakupatsani mwa Ambuye Yesu.


Pakutinso pamene tinali nanu tidakulamulirani ichi, Ngati munthu safuna kugwira ntchito, asadyenso.


Ndipo tikulamulirani, abale, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti mubwevuke kwa mbale yense wakuyenda dwakedwake, wosatsata mwambo umene anaulandira kwa ife.


kuti usunge lamulolo, lopanda banga, lopanda chilema, kufikira maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Khristu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa