Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 10:25 - Buku Lopatulika

25 Kumkwanira wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wake, ndi kapolo monga mbuye. Ngati anamutcha mwini banja Belezebulu, sadzaposa kodi kuwatero apabanja ake?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Kumkwanira wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wake, ndi kapolo monga mbuye. Ngati anamutcha mwini banja Belezebulu, sadzaposa kodi kuwatero apabanja ake?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Kumkwanira wophunzira kuti alingane ndi mphunzitsi wake, ndiponso wantchito kuti alingane ndi mbuye wake. Tsono ngati mwini banja anthu adamutcha Belezebulu, nanji a m'banja mwake, kodi sadzaŵatcha maina oipa koposa apa?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Nʼkoyenera kuti wophunzira akhale ngati mphunzitsi wake, ndi wantchito akhale ngati bwana wake. Ngati mwini banja atchedwa Belezebabu, koposa kotani a mʼnyumba mwake!

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 10:25
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Ahaziya anagwa kuchokera pamwamba pa chipinda chake chosanja chinali ku Samariya, nadwala, natuma mithenga, nanena nayo, Mufunsire kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni ngati ndidzachira nthenda iyi.


Koma Afarisi pakumva, anati, Uyu samatulutsa ziwanda koma ndi mphamvu yake ya Belezebulu, mkulu wa ziwanda.


Ndipo ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Belezebulu, ana anu amazitulutsa ndi mphamvu ya yani? Chifukwa chake iwo adzakhala oweruza anu.


Koma Afarisi analinkunena, Atulutsa ziwanda ndi mphamvu zake za mfumu ya ziwanda.


Ndipo anati kwa Iye, Tikhoza. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Chikho chimene ndimwera Ine mudzamwera; ndipo ubatizo umene ndibatizidwa nao Ine, mudzabatizidwa nao;


Ndipo alembi amene adatsika ku Yerusalemu ananena kuti, Ali naye Belezebulu, ndipo, Ndi mkulu wao wa ziwanda atulutsa ziwanda.


Koma ena mwa iwo anati, Ndi Belezebulu mkulu wa ziwanda amatulutsa ziwanda.


Ndiponso ngati Satana agawanika kudzitsutsa mwini, udzaimika bwanji ufumu wake? Popeza munena kuti nditulutsa ziwanda ndi Belezebulu.


Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi Belezebulu, ana anu azitulutsa ndi yani? Mwa ichi iwo adzakhala oweruza anu.


Koma ambiri mwa iwo ananena, Ali ndi chiwanda, nachita misala; mukumva Iye bwanji?


Khamu la anthu linayankha, Muli ndi chiwanda: afuna ndani kukuphani Inu?


Ayuda anayankha nati kwa Iye, Kodi sitinenetsa kuti Inu ndinu Msamariya, ndipo muli ndi chiwanda?


Ayuda anati kwa Iye, Tsopano tazindikira kuti muli ndi chiwanda. Abrahamu anamwalira, ndi aneneri; ndipo Inu munena, Munthu akasunga mau anga, sadzalawa imfa kunthawi yonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa