Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 79:9 - Buku Lopatulika

9 Tithandizeni Mulungu wa chipulumutso chathu, chifukwa cha ulemerero wa dzina lanu; ndipo tilanditseni, ndi kutifafanizira zoipa zathu, chifukwa cha dzina lanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Tithandizeni Mulungu wa chipulumutso chathu, chifukwa cha ulemerero wa dzina lanu; ndipo tilanditseni, ndi kutifafanizira zoipa zathu, chifukwa cha dzina lanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Tithandizeni, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, kuti dzina lanu likhale ndi ulemerero. Tipulumutseni, ndipo mutikhululukire zochimwa zathu, kuti dzina lanu lilemekezeke.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Tithandizeni Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, chifukwa cha ulemerero wa dzina lanu; tipulumutseni ndi kutikhululukira machimo athu chifukwa cha dzina lanu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 79:9
17 Mawu Ofanana  

Ndipo Asa anafuulira kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, palibe wina ngati Inu, kuthandiza pakati pa wamphamvu ndi iye wopanda mphamvu; tithandizeni Yehova Mulungu wathu, titama Inu, tatulukira aunyinji awa m'dzina lanu. Yehova, Inu ndinu Mulungu wathu, munthu asakukanikeni.


Kwa ife ai, Yehova, kwa ife ai, koma kwa dzina lanu patsani ulemerero, chifukwa cha chifundo chanu, ndi choonadi chanu.


Chifukwa cha dzina lanu, Yehova, ndikhululukireni kusakaza kwanga, pakuti ndiko kwakukulu.


Pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa; ndipo chifukwa cha dzina lanu ndiyendetseni bwino, ndipo nditsogolereni.


Mphulupulu zinandipambana; koma mudzafafaniza zolakwa zathu.


Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, chifukwa cha Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira machimo ako.


Chifukwa cha dzina langa ndidzachedwetsa mkwiyo wanga, ndi chifukwa cha kutamanda kwanga ndidzakulekerera, kuti ndisakuchotse.


Musatinyoze ife, chifukwa cha dzina lanu; musanyazitse mpando wachifumu wa ulemerero wanu; mukumbukire musasiye pangano lanu lopangana ndi ife.


Zingakhale zoipa zathu zititsutsa ife, chitani Inu chifukwa cha dzina lanu, Yehova; pakuti zobwerera zathu zachuluka; takuchimwirani Inu.


Koma ndinachichita chifukwa cha dzina langa, kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu amene ndinawatulutsa pamaso pao.


M'mwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova nditachita nanu chifukwa cha dzina langa, si monga mwa njira zanu zoipa, kapena monga mwa machitidwe anu ovunda, nyumba ya Israele inu, ati Ambuye Yehova.


Koma ndinachichita chifukwa cha dzina langa, kuti lisadetsedwe pamaso pa amitundu amene anakhala pakati pao, amene pamaso pao ndinadzidziwitsa kwa iwo, pakuwatulutsa m'dziko la Ejipito.


Ambuye, imvani; Ambuye khululukirani; Ambuye, mverani nimuchite; musachedwa, chifukwa cha inu nokha, Mulungu wanga; pakuti mzinda wanu ndi anthu anu anatchedwa dzina lanu.


Ambuye Mulungu wathu ndiye wachifundo, ndi wokhululukira; pakuti tampandukira Iye;


Mukapanda kumvera, mukapanda kuliika mumtima mwanu, kupatsa dzina langa ulemerero, ati Yehova wa makamu, ndidzakutumizirani temberero, ndi kutemberera madalitso anu; inde, ndawatemberera kale chifukwa simuliika mumtima.


kuti uyamikidwe ulemerero wa chisomo chake, chimene anatichitira ife kwaufulu mwa Wokondedwayo.


Akadzamva ichi Akanani ndi okhala m'dziko onse, adzatizinga ndi kuduliratu dzina lathu padziko lapansi; ndipo mudzachitiranji dzina lanu lalikulu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa