Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 73:25 - Buku Lopatulika

25 Ndili ndi yani Kumwamba, koma Inu? Ndipo padziko lapansi palibe wina wondikonda koma Inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Ndili ndi yani Kumwamba, koma Inu? Ndipo pa dziko lapansi palibe wina wondikonda koma Inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Nanga ndili ndi yani kumwamba kupatula Inu? Pansi pano palibe kanthu kena kamene ndimafuna, koma Inu nokha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Kodi kumwamba ndili ndi yani kupatula Inu? Ndipo dziko lapansi lilibe chilichonse chimene ndimachilakalaka koposa Inuyo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 73:25
19 Mawu Ofanana  

Pomlingirira Iye pandikonde; ndidzakondwera mwa Yehova.


Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.


Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Ambuye wanga, ndilibe chabwino china choposa Inu.


Yehova ndiye gawo la cholowa changa ndi chikho changa, ndinu wondigwirira cholandira changa.


Koma ine ndidzapenyerera nkhope yanu m'chilungamo, ndidzakhuta mtima ndi maonekedwe anu, pamene ndidzauka.


Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.


Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu, kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni, ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.


Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake; milomo yanga idzakulemekezani.


Pakuti kuli yani kuthambo timlinganize ndi Yehova? Afanana ndi Yehova ndani mwa ana a amphamvu?


Iye wakukonda atate wake, kapena amake koposa Ine, sayenera Ine, ndipo iye wakukonda mwana wake wamwamuna, kapena wamkazi koposa Ine, sayenera Ine.


Odala ali oyera mtima; chifukwa adzaona Mulungu.


Komatu zenizeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Khristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Khristu,


Okondedwa, tsopano tili ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, Pakuti tidzamuona Iye monga ali.


Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa