Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 73:13 - Buku Lopatulika

13 Indedi, ndinayeretsa mtima wanga kwachabe, ndipo ndinasamba m'manja mosalakwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Indedi, ndinayeretsa mtima wanga kwachabe, ndipo ndinasamba m'manja mosalakwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Ine ndasunga mtima wanga woyera, ndasamba m'manja kuwonetsa kuti ndine wosalakwa, koma zonsezi popanda phindu konse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ndithudi ine ndawusunga pachabe mtima wanga woyera; pachabe ndasamba mʼmanja mwanga mwa kusalakwa kwanga.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 73:13
12 Mawu Ofanana  

Wamphamvuyonse ndiye yani kuti timtumikire? Ndipo tidzapindulanji pakumpemphera Iye?


Pakuti anati, Munthu sapindula kanthu nako kuvomerezana naye Mulungu.


pakuti munena, Upindulanji nacho? Posachimwa ndinapindula chiyani chimene sindikadapindula pochimwa?


Ndikati, Ndidzaiwala chondidandaulitsa, ndidzasintha nkhope yanga yachisoni, ndidzasekerera.


Mlandu udzanditsutsa; potero ndigwire ntchito chabe chifukwa ninji?


Mudzandiviikanso muli zoola, ndi zovala zanga zidzanyansidwa nane.


Woyera m'manja, ndi woona m'mtima, ndiye; iye amene sanakweze moyo wake kutsata zachabe, ndipo salumbira monyenga.


Ndidzasamba manja anga mosalakwa; kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova;


Mundilengere mtima woyera, Mulungu; mukonze mzimu wokhazikika m'kati mwanga.


Mwanena, Kutumikira Mulungu nkwa chabe; ndipo tapindulanji ndi kusunga udikiro wake, ndi kuyenda ovala zamaliro pamaso pa Yehova wa makamu?


Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m'manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa