Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 69:27 - Buku Lopatulika

27 Onjezani mphulupulu pa mphulupulu zao; ndipo asafikire chilungamo chanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Onjezani mphulupulu pa mphulupulu zao; ndipo asafikire chilungamo chanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Muŵalange pa cholakwa chao chilichonse, musagamule kuti alibe mlandu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Awonjezereni kulakwa pa kulakwa kwawo, musalole kuti akhale ndi gawo pa chipulumutso chanu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 69:27
23 Mawu Ofanana  

ndipo musakwirira mphulupulu yao, ndi kulakwa kwao kusafafanizike pamaso panu; pakuti anautsa mkwiyo wanu pamaso pa omanga linga.


Mundilondola bwanji ngati Mulungu, losakukwanirani thupi langa?


Mphulupulu za makolo ake zikumbukike ndi Yehova; ndi tchimo la mai wake lisafafanizidwe.


Iye adzalandira dalitso kwa Yehova, ndi chilungamo kwa Mulungu wa chipulumutso chake.


Potero ndinawaperekera kuuma mtima kwao, ayende monga mwa uphungu waowao.


Koma pamene Farao anaona kuti panali kupuma, anaumitsa mtima wake, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.


Koma Farao anaumitsa mtima wake nthawi yomweyonso, ndipo sanalole anthu amuke.


Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, kuti sanamvere iwo; monga Yehova adalankhula ndi Mose.


Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira chilungamo; m'dziko la machitidwe oongoka, iye adzangochimwa, sadzaona chifumu cha Yehova.


ndipo ndidzaupasula; sudzadzomboleredwa kapena kulimidwa; koma padzamera lunguzi ndi minga; ndidzalamuliranso mitambo kuti isavumbwepo mvula.


Zoonadi Iye ananyamula zowawa zathu, ndi kusenza zisoni zathu; koma ife tinamuyesa wokhomedwa, wokanthidwa ndi Mulungu, ndi wovutidwa.


Ndipo otsala mwa inu adzazunzika m'moyo ndi mphulupulu zao m'maiko a adani anu; ndiponso ndi mphulupulu za makolo ao adzazunzika m'moyo.


Ndipo pakuona mkuyu umodzi panjira, anafika pamenepo, napeza palibe kanthu koma masamba okhaokha; nati Iye kwa uwo, Sudzabalanso chipatso kunthawi zonse. Ndipo pomwepo mkuyuwo unafota.


Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'chidziwitso chao, anawapereka Mulungu kumtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera;


Chotero Iye achitira chifundo amene Iye afuna, ndipo amene Iye afuna amuumitsa mtima.


koma Israele, potsata lamulo la chilungamo, sanafikile lamulolo.


Aleksandro wosula mkuwa anandichitira zoipa zambiri: adzambwezera iye Ambuye monga mwa ntchito zake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa