Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 50:16 - Buku Lopatulika

16 Koma kwa woipa Mulungu anena, Uli nao chiyani malemba anga kulalikira, ndi kutchula pangano langa pakamwa pako?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Koma kwa woipa Mulungu anena, Uli nao chiyani malemba anga kulalikira, ndi kutchula pangano langa pakamwa pako?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Koma kwa munthu woipa Mulungu amati, “Ukuvutikiranji ndi kutchula malamulo anga? Bwanji pakamwa pako pakulankhula za chipangano changa?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Koma kwa woyipa, Mulungu akuti, “Kodi uli ndi mphamvu yanji kuti uzinena malamulo anga kapena kutenga pangano langa pa milomo yako?

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 50:16
20 Mawu Ofanana  

Chinsinsi cha Yehova chili kwa iwo akumuopa Iye; ndipo adzawadziwitsa pangano lake.


Miyendo ya wopunduka ili yolobodoka, momwemo mwambi m'kamwa mwa zitsiru.


Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutali ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;


Kulibe mtendere, ati Yehova, kwa oipa.


Ndipo woipayo akatembenukira kuleka choipa chake adachichita, nakachita chiweruzo ndi chilungamo, adzapulumutsa moyo wake.


Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira Iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m'choonadi.


koma ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.


losati longa pangano ndinalichita ndi makolo ao, tsikuli ndinawagwira kudzanja iwo kuwatsogolera atuluke m'dziko la Ejipito; kuti iwo sanakhalebe m'pangano langa, ndipo Ine sindinawasamalire iwo, anena Ambuye.


posiya njira yolunjika, anasokera, atatsata njira ya Balamu mwana wa Beori, amene anakonda mphotho ya chosalungama;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa