Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 37:10 - Buku Lopatulika

10 Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti; inde, udzayang'anira mbuto yake, nudzapeza palibe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti; inde, udzayang'anira mbuto yake, nudzapeza palibe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Kanthaŵi pang'ono ndipo munthu woipa sadzakhalaponso, ngakhale muyang'ane bwino pamalo pamene analiri, simudzampezapo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Kwa kanthawi oyipa sadzapezekanso; ngakhale muwafunefune, sadzapezekanso.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 37:10
25 Mawu Ofanana  

Nati Yehu kwa Bidikara kazembe wake, Mnyamule, numponye m'munda wa Naboti wa ku Yezireele; pakuti kumbukira m'mene ine ndi iwe tinali pa akavalo athu pamodzi kutsata Ahabu atate wake, Yehova anamsenzetsa katundu uyu.


Nampachika Hamani pa mtengo adaukonzera Mordekai. Pamenepo mkwiyo wa mfumu unatsika.


Koma munthu akufa atachita liondeonde inde, munthu apereka mzimu wake, ndipo ali kuti?


kuti kufuula kokondwera kwa woipa sikukhalira kutha, ndi chimwemwe cha wonyoza Mulungu chikhala kamphindi?


Akwezeka; m'kamphindi kuli zii; inde atsitsidwa, achotsedwa monga ena onse, adulidwa ngati tirigu ngala zake.


Sadzabweranso kunyumba yake, osamdziwanso malo ake.


Mulekeranji kukhululukira kulakwa kwanga ndi kundichotsera mphulupulu yanga? Popeza tsopano ndidzagona kufumbi; mudzandifunafuna, koma ine palibe.


Pakuti mphepo ikapitapo pakhala palibe: Ndi malo ake salidziwanso.


Pakuti aona anzeru amafa, monga aonongekera wopusa, wodyerera momwemo, nasiyira ena chuma chao.


Potero Mulungu adzakupasula kunthawi zonse, adzakuchotsa nadzakukwatula m'hema mwako, nadzakuzula, kukuchotsa m'dziko la amoyo.


Nyumba ya oipa idzapasuka; koma hema wa oongoka mtima adzakula.


Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m'mapemphero;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa