Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 25:4 - Buku Lopatulika

4 Mundidziwitse njira zanu, Yehova; Mundiphunzitse mayendedwe anu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Mundidziwitse njira zanu, Yehova; Mundiphunzitse mayendedwe anu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mundidziŵitse njira zanu, Inu Chauta, mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndidziwitseni njira zanu Inu Yehova, phunzitseni mayendedwe anu;

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 25:4
11 Mawu Ofanana  

pamenepo mverani Inu mu Mwamba, ndi kukhululukira tchimo la akapolo anu, ndi la anthu anu Aisraele; pakuti muwaphunzitsa njira yokoma ayenera kuyendamo, ndi kupatsa mvula padziko lanu, limene munawapatsa anthu anu likhale cholowa chao.


Mundizindikiritse njira ya malangizo anu; kuti ndilingalire zodabwitsa zanu.


Mundimvetse chifundo chanu mamawa; popeza ndikhulupirira Inu: Mundidziwitse njira ndiyendemo; popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.


Mundiphunzitse njira yanu, Yehova, munditsogolere panjira yachidikha, chifukwa cha adani anga.


Mverani mau anga, Yehova, Zindikirani kulingirira kwanga.


Yehova, munditsogolere m'chilungamo chanu, chifukwa cha akundizondawo; mulungamitse njira yanu pamaso panga.


Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m'choonadi chanu, muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.


Ndipo tsopano, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, mundidziwitsetu njira zanu, kuti ndikudziweni, ndi kuti ndipeze ufulu pamaso panu; ndipo penyani kuti mtundu uwu ndi anthu anu.


Ndimayenda m'njira ya chilungamo, pakati pa mayendedwe a chiweruzo,


Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m'mayendedwe ake; chifukwa mu Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mau a Yehova kuchokera mu Yerusalemu.


Yehova atero, Imani m'njira ndi kuona, funsani za mayendedwe akale, m'menemo muli njira yabwino, muyende m'menemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu; koma anati, Sitidzayendamo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa