Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 139:21 - Buku Lopatulika

21 Kodi sindidana nao iwo akudana ndi Inu, Yehova? Ndipo kodi sindimva nao chisoni iwo akuukira Inu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Kodi sindidana nao iwo akudana ndi Inu, Yehova? Ndipo kodi sindimva nao chisoni iwo akuukira Inu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Kodi sindidana nawo anthu odana nanu, Inu Chauta? Kodi sindinyansidwa nawo anthu okuukirani?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Kodi ine sindidana nawo amene amakudani, Inu Yehova? Kodi sindinyansidwa nawo amene amakuwukirani?

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 139:21
12 Mawu Ofanana  

Natuluka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza zoipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova.


Maso anga atsitsa mitsinje ya madzi, popeza sasamalira chilamulo chanu.


Ndinapenya ochita monyenga, ndipo ndinanyansidwa nao; popeza sasamalira mau anu.


M'maso mwake munthu woonongeka anyozeka; koma awachitira ulemu akuopa Yehova. Atalumbira kwa tsoka lake, sasintha ai.


Ndidana nao msonkhano wa ochimwa, ndipo sindidzakhala nao pansi ochita zoipa.


Ndikwiya nao iwo akusamala zachabe zonama, koma ndikhulupirira Yehova.


Koma ngati simudzamva, moyo wanga udzalira m'tseri chifukwa cha kunyada kwanu; diso langa lidzalira kwambiri, lidzagwa misozi, chifukwa zoweta za Yehova zagwidwa m'nsinga.


Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake.


Ndipo m'mene anayandikira, anaona mzindawo naulirira,


Ndidziwa ntchito zako, ndi chilemetso chako ndi chipiriro chako ndi kuti sungathe kulola oipa, ndipo unayesa iwo amene adzitcha okha atumwi, osakhala atumwi, nuwapeza onama;


Koma ichi uli nacho, kuti udana nazo ntchito za Anikolai, zimene Inenso ndidana nazo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa