Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 9:43 - Buku Lopatulika

43 Ndipo ngati dzanja lako likulakwitsa iwe, ulidule: nkwabwino kwa iwe kulowa m'moyo wopunduka dzanja, koposa kukhala ndi manja ako awiri ndi kulowa mu Gehena, m'moto wosazima.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

43 Ndipo ngati dzanja lako likulakwitsa iwe, ulidule: nkwabwino kwa iwe kulowa m'moyo wopunduka dzanja, koposa kukhala ndi manja ako awiri ndi kulowa m'Gehena, m'moto wosazima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

43 Tsono ngati dzanja lako likuchimwitsa, lidule. Ndi bwino kuti ukaloŵe ku moyo wosatha uli woduka dzanja, kupambana kuti ukaloŵe uli ndi manja onse aŵiri ku Gehena, kwa moto wosazimika.” [

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

43 Ngati dzanja lako likuchimwitsa, lidule. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa mʼmoyo ndi dzanja limodzi kusiyana ndi kukhala ndi manja awiri ndi kupita ku gehena, kumene moto wake suzima.

Onani mutuwo Koperani




Marko 9:43
23 Mawu Ofanana  

chinkana achisunga, osachileka, nachikhalitsa m'kamwa mwake;


Ndimo wamphamvu adzakhala ngati chingwe chathonje, ndi ntchito yake ngati nthethe; ndipo zonse zidzayaka moto pamodzi, opanda wozimitsa.


Mudzidulire nokha kwa Yehova, chotsani khungu la mitima yanu, amuna inu a Yuda ndi okhala mu Yerusalemu; ukali wanga ungatuluke ngati moto, ungatenthe kuti sangathe kuuzima, chifukwa cha kuipa kwa machitidwe anu.


Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuitole nsomba yoyamba kuwedza; ndipo ukaikanula pakamwa pake udzapezamo rupiya; tatenga limeneli, nuwapatse ilo pamutu pa iwe ndi Ine.


Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake:


chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.


koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.


Koma pamene ukonza phwando uitane aumphawi, opunduka, otsimphina, akhungu;


Ndipo kapoloyo pakubwera anauza mbuye wake zinthu izi. Pamenepo mwini nyumba anakwiya, nati kwa kapolo wake, Tuluka msanga, pita kumakwalala ndi kunjira za mzinda, nubwere nao muno aumphawi ndi opunduka ndi akhungu ndi otsimphina.


amene chouluzira chake chili m'dzanja lake, kuti ayeretse padwale pake, ndi kusonkhanitsa tirigu m'nkhokwe yake; koma mankhusu adzatentha m'moto wosazima.


pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zochita zake za thupi, mudzakhala ndi moyo.


koma ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.


Koma iwo a Khristu Yesu adapachika thupi, ndi zokhumba zake, ndi zilakolako zake.


Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano;


ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m'dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza;


Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu,


Momwemo pakutaya choipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kaduka, ndi masinjiriro onse,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa