Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 9:42 - Buku Lopatulika

42 Ndipo yense amene adzalakwitsa kamodzi ka tiana timeneto takukhulupirira Ine, kuli kwabwino kwa iye makamaka kuti mwala waukulu wamphero ukolowekedwe m'khosi mwake, naponyedwe iye m'nyanja.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

42 Ndipo yense amene adzalakwitsa kamodzi ka tiana timeneto takukhulupirira Ine, kuli kwabwino kwa iye makamaka kuti mwala waukulu wamphero ukolowekedwe m'khosi mwake, naponyedwe iye m'nyanja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

42 “Aliyense wochimwitsa ngakhale mmodzi mwa ana okhulupirira Ineŵa, ameneyo kukadakhala kwabwino koposa kuti ammangirire chimwala cha mphero m'khosi ndi kukamuponya m'nyanja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

42 “Ndipo ngati wina aliyense achimwitsa mmodzi wa ana angʼono awa amene akhulupirira Ine, kukanakhala bwino kwa iye kuti aponyedwe mʼnyanja atamangiriridwa mwala waukulu mʼkhosi mwake.

Onani mutuwo Koperani




Marko 9:42
19 Mawu Ofanana  

Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuitole nsomba yoyamba kuwedza; ndipo ukaikanula pakamwa pake udzapezamo rupiya; tatenga limeneli, nuwapatse ilo pamutu pa iwe ndi Ine.


Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.


koma yense amene adzakhumudwitsa kamodzi ka tiana iti, takukhulupirira Ine, kumuyenera iye kuti mphero yaikulu ikolowekedwe m'khosi mwake, namizidwe poya pa nyanja.


ndipo anagwa pansi, namva mau akunena naye, Saulo, Saulo, Undilondalonderanji?


Chifukwa chake tisaweruzanenso wina mnzake; koma weruzani ichi makamaka, kuti munthu asaike chokhumudwitsa panjira ya mbale wake, kapena chomphunthwitsa.


Koma monga kwalembedwa, Iwo amene uthenga wake sunawafikire, adzaona, ndipo iwo amene sanamve, adzadziwitsa.


Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang'anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo.


osapatsa chokhumudwitsa konse m'chinthu chilichonse, kuti utumikiwo usanenezedwe;


kuti mukayese inu zinthu zosiyana; kuti mukakhale a mtima woona ndi wosalakwa, kufikira tsiku la Khristu;


Chifukwa chake nditi akwatiwe amasiye aang'ono, nabale ana, naweruzire nyumba, osapatsa chifukwa kwa mdaniyo chakulalatira;


Ndipo ambiri adzatsata zonyansa zao; chifukwa cha iwo njira ya choonadi idzanenedwa zamwano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa