Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 8:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo anamgwira dzanja munthu wakhunguyo, natulukira naye kunja kwa mudzi; ndipo atamthira malovu m'maso mwake, naika manja pa iye, anamfunsa, Uona kanthu kodi?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo anamgwira dzanja munthu wakhunguyo, natulukira naye kunja kwa mudzi; ndipo atamthira malovu m'maso mwake, naika manja pa iye, anamfunsa, Uona kanthu kodi?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Yesu adamgwira dzanja, natuluka naye kunja kwa mudzi. Adapaka malovu m'maso mwa munthuyo, namsanjika manja nkumufunsa kuti, “Kodi ukuwona kanthu?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Iye anagwira dzanja la munthu wosaonayo napita naye kunja kwa mudzi. Atalavulira mʼmaso a munthuyo ndi kumusanjika manja, Yesu anafunsa kuti, “Kodi ukuona kalikonse?”

Onani mutuwo Koperani




Marko 8:23
12 Mawu Ofanana  

atero Yehova, amene anakutenga iwe, nakuumba kuchokera m'mimba, amene adzathangata iwe. Usaope Yakobo, mtumiki wanga ndi iwe, Yesuruni, amene ndakusankha iwe.


Palibenso wina wakumtsogolera mwa ana aamuna onse, amene iye anawabala; palibe wina amgwira dzanja mwa ana onse anawalera.


si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo ao tsiku lija ndinawagwira manja kuwatulutsa m'dziko la Ejipito; pangano langa limenelo analiswa, ngakhale ndinali mbuyao, ati Yehova.


nanena, kuti, Kamwana kanga kabuthu kalinkutsirizika; ndikupemphani Inu mufikeko, muike manja anu pa iko, kuti kapulumuke, ndi kukhala ndi moyo.


Ndipo anampatula pa khamu la anthu pa yekha, nalonga zala zake m'makutu mwake, nalavula malovu, nakhudza lilime lake:


Ndipo anakweza maso, nanena, Ndiona anthu; pakuti ndiwapenya ayendayenda ngati mitengo.


Ndipo anamtumiza amuke kwao, nanena, Usalowe konse m'mudzi.


Ndipo kapitao wamkulu anamgwira dzanja, napita naye padera, namfunsa m'tseri, Chiyani ichi uli nacho kundifotokozera?


Ndipo Saulo anauka; koma potseguka maso ake, sanapenye kanthu; ndipo anamgwira dzanja, namtenga nalowa naye mu Damasiko.


losati longa pangano ndinalichita ndi makolo ao, tsikuli ndinawagwira kudzanja iwo kuwatsogolera atuluke m'dziko la Ejipito; kuti iwo sanakhalebe m'pangano langa, ndipo Ine sindinawasamalire iwo, anena Ambuye.


ndikulangiza ugule kwa Ine golide woyengeka m'moto, kuti ukakhale wachuma, ndi zovala zoyera, kuti ukadziveke, ndi kuti manyazi a usiwa wako asaoneke; ndi mankhwala opaka m'maso mwako, kuti ukaone.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa