Marko 5:4 - Buku Lopatulika4 pakuti ankamangidwa kawirikawiri ndi matangadza ndi maunyolo, ndipo anamwetula maunyolo, naduladula matangadza; ndipo palibe munthu anali ndi mphamvu yakumfuya. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 pakuti ankamangidwa kawirikawiri ndi matangadza ndi maunyolo, ndipo anamwetula maunyolo, naduladula matangadza; ndipo palibe munthu anali ndi mphamvu yakumfuya. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Kale anthu adaayesa kangapo kummanga miyendo ndi zitsulo, ndiponso kummanga manja ndi maunyolo, koma iye ankangoŵamwetsula maunyolowo, ndipo zitsulo zomanga miyendozo ankangozithyola. Padaalibe ndi mmodzi yemwe wotha kumgonjetsa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Pakuti nthawi zambiri akamumanga manja ndi miyendo amadula maunyolo ndi kudula zitsulo zimene zinali mʼmapazi ake. Panalibe amene anali ndi mphamvu yoti ndi kumugonjetsa. Onani mutuwo |