Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 4:24 - Buku Lopatulika

24 Ndipo ananena nao, Yang'anirani chimene mukumva; ndi muyeso umene muyesera nao udzayesedwa kwa inu; ndipo kudzaonjezedwa kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Ndipo ananena nao, Yang'anirani chimene mukumva; ndi muyeso umene muyesera nao udzayesedwa kwa inu; ndipo kudzaonjezedwa kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Adaŵauzanso kuti, “Muzisamala pa mau amene mumamva. Muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu, ndipo inuyo adzakubzoletserani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Anapitiriza nati, “Ganizirani mosamala zimene mukumva, ndi muyeso umene mugwiritsa ntchito, mudzayesedwa nawo, ndipo ngakhale kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Marko 4:24
16 Mawu Ofanana  

Ukangofuna, mwananga, kusochera kusiya mau akudziwitsa, leka kumva mwambo.


Tcherani khutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzapangana nanu chipangano chosatha, ndicho zifundo zoona za Davide.


atero Yehova: Tadzayang'anirani nokha, musanyamule katundu tsiku la Sabata, musalowe naye pa zipata za Yerusalemu;


Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso.


Ndipo panadza mtambo wakuwaphimba iwo; ndipo mau munatuluka m'mtambomo, kuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa; mverani Iye.


Chifukwa chake yang'anirani mamvedwe anu; pakuti kudzapatsidwa kwa iye amene ali nacho; ndipo kwa iye amene alibe chidzachotsedwa, chingakhale chija aoneka ngati ali nacho.


Ndipo nkhosa zina ndili nazo, zimene sizili za khola ili; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mau anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi.


Nkhosa zanga zimva mau anga, ndipo Ine ndizizindikira, ndipo zinditsata Ine.


Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo ilipo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo.


Amenewa anali mfulu koposa a mu Tesalonika, popeza analandira mau ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m'malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.


Koma nditi ichi, kuti iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta. Ndipo iye wakufesa moolowa manja, moolowa manjanso adzatuta.


Mwa ichi tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo.


lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nao kufikira chipulumutso;


Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m'dziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa