Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 4:12 - Buku Lopatulika

12 kuti kupenya apenye, koma asazindikire; ndipo kumva amve, koma asadziwitse; kuti pena angatembenuke, ndi kukhululukidwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 kuti kupenya apenye, koma asazindikire; ndipo kumva amve, koma asadziwitse; kuti pena angatembenuke, ndi kukhululukidwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 kuti choncho, monga mau a Mulungu aja amanena, “ ‘Kuyang'ana ayang'ane ndithu, koma asapenye kanthu, ndipo kumva amve ndithu, koma asamvetse kanthu, kuti angatembenuke mtima, ndipo Mulungu angaŵakhululukire.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 kotero kuti, “ ‘Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu, kumva mudzamva koma osamvetsetsa, kuti mwina angatembenuke ndi kukhululukidwa!’ ”

Onani mutuwo Koperani




Marko 4:12
18 Mawu Ofanana  

Tulutsani anthu akhungu, amene ali ndi maso, ndi agonthi, amene ali ndi makutu.


Iwo sadziwa, kapena kuzindikira, chifukwa pamaso mwao papakidwa thope, kuti sangaone, ndi m'mitima mwako kuti sangadziwitse.


Kapena nyumba ya Yuda idzamva choipa chonse chimene nditi ndidzawachitire; kuti abwerere yense kuleka njira yake yoipa; kuti ndikhululukire mphulupulu yao ndi tchimo lao.


Tamvanitu ichi, inu anthu opusa, ndi opanda nzeru; ali ndi maso koma osaona, ali ndi makutu koma osamva;


Wobadwa ndi munthu iwe, ukhala pakati pa nyumba yampanduko, yokhala nao maso akuonera, koma osaona; ndi makutu akumvera, koma osamva; pakuti iwo ndiwo nyumba yampanduko.


Pokhala nao maso simupenya kodi? Ndi pokhala nao makutu simukumva kodi? Ndipo simukumbukira kodi?


Ndipo Iye anati, Kwapatsidwa kwa inu kuzindikira zinsinsi za Ufumu wa Mulungu; koma kwa ena otsala ndinena nao mwa mafanizo; kuti pakuona sangaone, ndi pakumva sangadziwitse.


Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera kunkhope ya Ambuye;


koma Yehova sanakupatseni mtima wakudziwa, ndi maso akupenya, ndi makutu akumva, kufikira lero lino.


wolangiza iwo akutsutsana mofatsa; ngati kapena Mulungu awapatse iwo chitembenuziro, kukazindikira choonadi,


koma anagwa m'chisokero; popeza adzipachikiranso okha Mwana wa Mulungu, namchititsa manyazi poyera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa