Marko 2:4 - Buku Lopatulika4 Ndipo pamene sanakhoze kufika kuli Iye, chifukwa cha khamu la anthu, anasasula tsindwi pokhala Iye; ndipo pamene anatha kuliboola, anatsitsa mphasa m'mene alinkugonamo wodwala manjenjeyo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Ndipo pamene sanakhoze kufika kuli Iye, chifukwa cha khamu la anthu, anasasula chindwi pokhala Iye; ndipo pamene anatha kuliboola, anatsitsa mphasa m'mene alinkugonamo wodwala manjenjeyo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Koma sadathe kufika naye pafupi ndi Yesuyo chifukwa cha kuchuluka kwa anthu. Choncho adakwera pa denga, nangosasula dengalo kuyang'anana ndi pamene Yesu analiri, nkutsitsira pachiboopo machira amene adaanyamulira munthu uja. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Popeza sakanatha kufika naye kwa Yesu chifukwa cha gulu la anthu, anasasula denga chapamwamba pamene panali Yesu, ndipo atabowoleza, anatsitsa mphasa yomwe munthu wofa ziwaloyo anagonapo. Onani mutuwo |