Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 2:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo palibe munthu amatsanulira vinyo watsopano m'matumba akale: pena vinyo adzaphulitsa matumba, ndipo aonongeka vinyo, ndi matumba omwe: koma vinyo watsopano amatsanulira m'matumba atsopano.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo palibe munthu amatsanulira vinyo watsopano m'matumba akale: pena vinyo adzaphulitsa matumba, ndipo aonongeka vinyo, ndi matumba omwe: koma vinyo watsopano amatsanulira m'matumba atsopano.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Ndiponso munthu sathira vinyo watsopano m'matumba achikopa akale. Chifukwa akatero, vinyoyo amaphulitsa matumba aja, ndipo choncho vinyo uja amatayika, matumbawo nkutha ntchito. Koma vinyo watsopano amamuthira m'matumba atsopanonso.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Ndipo palibe amene amathira vinyo watsopano mʼmatumba akale a vinyo. Ngati atatero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa matumba a vinyo ndipo vinyoyo pamodzi ndi matumbawo zidzawonongeka. Ayi, satero, amathira vinyo watsopano mʼmatumba atsopanonso.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 2:22
9 Mawu Ofanana  

Taonani, m'chifuwa mwanga muli ngati vinyo wosowa popungulira, ngati matumba atsopano akuti aphulike.


Mtima wanga ukhale wangwiro m'malemba anu; kuti ndisachite manyazi.


Popeza ndakhala ngati thumba lofukirira; koma sindiiwala malemba anu.


Kapena samathira vinyo watsopano m'matumba akale; akatero, matumba aphulika, ndi vinyo atayika, ndi matumba aonongeka; koma athira vinyo watsopano m'matumba atsopano, ndi zonse ziwiri zisungika.


Palibe munthu asokerera chigamba cha nsalu yaiwisi pa chofunda chakale; pena chimene choti chidzakonza chizomolapo, chatsopanocho chizomoka pa chakalecho, ndipo chiboo chikulapo.


Ndipo kunali kuti anapita Iye pakati pa minda tsiku la Sabata; ndipo ophunzira ake poyenda anayamba kubudula ngala za dzinthu.


ndi matumba a vinyo awa tinawadzaza akali atsopano; ndipo taonani, ang'ambika; ndi malaya athu awa ndi nsapato zathu zatha, chifukwa cha ulendo wochokera kutali ndithu.


zinachita momchenjerera, ndipo zinapita mooneka ngati mithenga, ndipo zinatenga matumba akale pa abulu ao, ndi matumba a vinyo akale ndi ong'ambika ndi omangamanga;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa