Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 2:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo alembi a kwa Afarisi, pakuona kuti alinkudya nao ochimwa ndi amisonkho, ananena ndi ophunzira ake, Uyu akudya ndi kumwa nao amisonkho ndi ochimwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo alembi a kwa Afarisi, pakuona kuti alinkudya nao ochimwa ndi amisonkho, ananena ndi ophunzira ake, Uyu akudya ndi kumwa nao amisonkho ndi ochimwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Pamene aphunzitsi a Malamulo a m'gulu la Afarisi adaona kuti Yesu akudya ndi anthu ochimwa, ndiponso ndi anthu okhometsa msonkho, adafunsa ophunzira ake kuti, “Bwanji akudya pamodzi ndi okhometsa msonkho ndiponso ndi anthu ochimwa?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Pamene aphunzitsi amalamulo a Afarisi anamuona akudya ndi “ochimwa” ndi amisonkho, anafunsa ophunzira ake kuti, “Chifukwa chiyani amadya ndi olandira msonkho ndi ochimwa?”

Onani mutuwo Koperani




Marko 2:16
14 Mawu Ofanana  

amene ati, Ima pa wekha, usadze chifupi ndi ine, pakuti ine ndili woyera kupambana iwe; amenewa ndiwo utsi m'mphuno mwanga, moto woyaka tsiku lonse.


Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.


Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho?


Ndipo Afarisi, pakuona ichi, ananena kwa ophunzira ake, Chifukwa ninji Mphunzitsi wanu alinkudya pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?


Ndipo ananyamuka namtsata Iye. Ndipo kunali kuti anakhala pakudya m'nyumba mwake, ndipo amisonkho ndi ochimwa ambiri anakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake, pakuti anali ambiri, ndipo anamtsata Iye.


Munthu amene atero bwanji? Achita mwano; akhoza ndani kukhululukira machimo, koma mmodzi, ndiye Mulungu?


Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindili monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, achigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu;


Pakuti Mwana wa Munthu anadza kufunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.


Ndipo m'mene anachiona anadandaula onse, nanena, Analowa amchereze munthu ali wochimwa.


Ndipo Afarisi ndi alembi ao anang'ung'udza kwa ophunzira ake, nanena, kuti, Bwanji inu mukudya ndi kumwa pamodzi ndi anthu amisonkho ndi ochimwa?


Ndipo chidauka chipolowe chachikulu, ndipo alembi ena a kwa Afarisi anaimirira, natsutsana, nanena, Sitipeza choipa chilichonse mwa munthuyu; ndipo nanga bwanji ngati mzimu kapena mngelo walankhula naye?


Koma iye amene ali wauzimu ayesa zonse, koma iye yekha sayesedwa ndi mmodzi yense.


Pakuti talingirirani Iye amene adapirira ndi ochimwa otsutsana naye kotere, kuti mungaleme ndi kukomoka m'moyo mwanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa