Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 2:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo ananyamuka namtsata Iye. Ndipo kunali kuti anakhala pakudya m'nyumba mwake, ndipo amisonkho ndi ochimwa ambiri anakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake, pakuti anali ambiri, ndipo anamtsata Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo ananyamuka namtsata Iye. Ndipo kunali kuti anakhala pakudya m'nyumba mwake, ndipo amisonkho ndi ochimwa ambiri anakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake, pakuti anali ambiri, ndipo anamtsata Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Tsono pamene Yesu ankadya m'nyumba mwa Leviyo, panali anthu ambiri okhometsa msonkho ndi anthu ochimwa, odzadya nao ndi Yesuyo ndi ophunzira ake. Anali anthu ambiri ndithu amene adaatsagana naye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Yesu atakalandira chakudya ku nyumba kwa Levi, amisonkho ambiri ndi “ochimwa” ankadya naye pamodzi ndi ophunzira ake, pakuti anali ambiri amene anamutsatira.

Onani mutuwo Koperani




Marko 2:15
8 Mawu Ofanana  

Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho?


Ndipo pakumuka, naona Levi mwana wa Alifeyo alikukhala polandirira msonkho, ndipo ananena naye, Tsata Ine.


Ndipo alembi a kwa Afarisi, pakuona kuti alinkudya nao ochimwa ndi amisonkho, ananena ndi ophunzira ake, Uyu akudya ndi kumwa nao amisonkho ndi ochimwa.


Koma amisonkho onse ndi anthu ochimwa analikumyandikira kudzamva Iye.


Ndipo Iye anatsika nao, naima pachidikha, ndi khamu lalikulu la ophunzira ake, ndi unyinji waukulu wa anthu a ku Yudeya yense ndi Yerusalemu, ndi a ku mbali ya nyanja ya ku Tiro ndi Sidoni, amene anadza kudzamva Iye ndi kudzachiritsidwa nthenda zao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa