Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 10:43 - Buku Lopatulika

43 Koma mwa inu sikutero ai; koma aliyense amene afuna kukhala wamkulu mwa inu adzakhala mtumiki wanu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

43 Koma mwa inu sikutero ai; koma amene aliyense afuna kukhala wamkulu mwa inu adzakhala mtumiki wanu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

43 Koma pakati pa inu zisamatero ai. Aliyense wofuna kukhala mkulu pakati panu, azikhala mtumiki wanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

43 Sizili choncho ndi inu. Mʼmalo mwake, amene akufuna kukhala wamkulu pakati panu ayenera kukhala wotumikira,

Onani mutuwo Koperani




Marko 10:43
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Yesu anawaitana, nanena nao, Mudziwa kuti iwo amene ayesedwa ambuye a mitundu ya anthu amachita ufumu pa iwo; ndipo akulu ao amachita ulamuliro pa iwo.


ndipo aliyense amene afuna kukhala woyamba mwa inu adzakhala kapolo wa onse.


Ndipo m'mene anakhala pansi anaitana khumi ndi awiriwo; nanena nao, Ngati munthu afuna kukhala woyamba, akhale wakuthungo wa onse, ndi mtumiki wa onse.


Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.


Ndinena ndi inu, anatsikira kunyumba kwake woyesedwa wolungama uyutu, wosati uja ai; pakuti yense wakudzikuza yekha adzachepetsedwa; koma wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa.


Koma sipadzatero ndi inu; komatu iye ali wamkulu mwa inu, akhale ngati wamng'ono; ndi iye ali woyamba, akhale ngati wotumikira.


Amene aliyense akalandire kamwana aka m'dzina langa alandira Ine; ndipo amene andilandira Ine alandira Iye amene anandituma Ine; pakuti iye wakukhala wamng'onong'ono wa inu nonse, yemweyu ndiye wamkulu.


Yesu anayankha, Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno.


Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.


Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa