Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Maliro 1:3 - Buku Lopatulika

3 Yuda watengedwa ndende chifukwa cha msauko ndi ukapolo waukulu; akhala mwa amitundu, sapeza popuma; onse akumlondola anampeza pakati popsinjikiza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Yuda watengedwa ndende chifukwa cha msauko ndi ukapolo waukulu; akhala mwa amitundu, sapeza popuma; onse akumlondola anampeza pakati popsinjikiza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ayuda apita ku ukapolo kukazunzika, ndi kukagwira ntchito yakalavulagaga. Akukhala m'maiko ena, osaona malo opumulira. Onse oŵapirikitsa aŵapeza, ali pa mavuto zedi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Yuda watengedwa ku ukapolo, kukazunzika ndi kukagwira ntchito yolemetsa. Iye akukhala pakati pa anthu a mitundu ina; ndipo alibe malo opumulira. Onse omuthamangitsa iye amupitirira, ndipo alibe kwina kothawira.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 1:3
22 Mawu Ofanana  

Ndi anthu otsalira m'mzinda, ndi opanduka akuthawira kwa mfumu ya Babiloni, ndi aunyinji otsalira, Nebuzaradani mkulu wa olindirira anamuka nao andende.


Niwakantha mfumu ya Babiloni, niwaphera ku Ribula m'dziko la Hamati. Motero anamuka nao Ayuda andende kuwachotsa m'dziko lao.


Pamenepo linga la mzindawo linagamulidwa, nathawira ankhondo onse usiku, njira ya ku chipata cha pakati pa makoma awiri, ili ku munda wa mfumu; Ababiloni tsono anali pamzinda pouzinga; nimuka mfumu panjira ya kuchidikha.


Koma nkhondo ya Ababiloni inalondola mfumu, nayipeza m'zidikha za Yeriko; koma nkhondo yake yonse inambalalikira.


Mizinda ya kumwera yatsekedwa, palibe wotsegulira. Yuda yense wachotsedwa m'ndende yenseyo, wachotsedwa m'nsinga.


Taonani, ndidzaitana akugwira nsomba ambiri, ati Yehova, ndipo adzawagwira iwo, pambuyo pake ndidzaitana osaka nyama ambiri, ndipo adzasaka iwo m'mapiri onse, ndi pa zitunda zonse, ndiponso m'mapanga a m'matanthwe.


Ndipo ndidzawapatsa akhale choopsetsa choipa ku maufumu a dziko lapansi; akhale chitonzo ndi nkhani ndi choseketsa, ndi chitemberero, monse m'mene ndidzawapirikitsiramo.


Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga anthu otsalira m'mzinda, ndi othawa omwe, opandukira, ndi kumtsata ndi anthu otsalira nanka nao am'nsinga ku Babiloni.


Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga ndende anthu aumphawi, ndi anthu otsala amene anatsala m'mzinda, ndi amene anapandukira, kutsata mfumu ya ku Babiloni, ndi otsala a unyinjiwo.


Koma nkhondo ya Ababiloni inamtsata mfumu, nimpeza Zedekiya m'zidikha za ku Yeriko; ndipo nkhondo yake yonse inambalalikira iye.


Zipata zake zalowa pansi; waononga ndi kuthyola mipiringidzo yake; mfumu yake ndi akalonga ake ali pakati pa amitundu akusowa chilamulo; inde, aneneri ake samalandira masomphenya kwa Yehova.


Amafuula kwa iwo, Chokani, osakonzeka inu, chokani, chokani, musakhudze kanthu. Pothawa iwo ndi kusochera, anthu anati kwa amitundu, Sadzagoneranso kuno.


Otilondola atigwira pakhosi pathu, tatopa osaona popumira.


Limodzi la magawo atatu la iwe lidzafa ndi mliri, nilidzatha ndi njala pakati pa iwe; ndi limodzi lidzagwa ndi lupanga pozinga pako; ndi limodzi ndidzalibalalikitsa kumphepo zonse, ndi kuwasololera lupanga lakuwatsata.


chifukwa chake mudzatumikira adani anu amene Yehova adzakutumizirani, ndi njala, ndi ludzu, ndi usiwa, ndi kusowa zinthu zonse; ndipo adzaika goli lachitsulo pakhosi panu, kufikira atakuonongani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa