Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Malaki 2:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo tsono, ansembe inu, lamulo ili ndi la kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo tsono, ansembe inu, lamulo ili ndi la kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Tsono ansembe inu, lamulo ili nlokhalira inu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 “Tsono chenjezo ili ndi la inu, inu ansembe.”

Onani mutuwo Koperani




Malaki 2:1
6 Mawu Ofanana  

Ndipo udzati kwa iwo, Atero Yehova, Taonani, ndidzadzaza ndi chiledzero onse okhala m'dziko muno, ngakhale mafumu onse amene akhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi onse okhala mu Yerusalemu.


Ndicho chifukwa cha machimo a aneneri ndi mphulupulu za ansembe ake, amene anakhetsa mwazi wa olungama pakati pake.


Imvani ichi, ansembe inu; mverani, inu nyumba ya Israele; tcherani khutu, inu nyumba ya mfumu; pakuti chiweruzochi chinena inu; pakuti munakhala msampha ku Mizipa, ndi ukonde woyalidwa pa Tabori.


Koma wotembereredwa wonyengayo, wokhala nayo yaimuna m'gulu lake, nawinda, naphera Yehova nsembe chinthu chachilema; pakuti Ine ndine mfumu yaikulu, ati Yehova wa makamu; ndipo dzina langa ndi loopsa pakati pa amitundu.


Mwana alemekeza atate wake, ndi mnyamata mbuye wake; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? Ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? Ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani?


Mukapanda kumvera, mukapanda kuliika mumtima mwanu, kupatsa dzina langa ulemerero, ati Yehova wa makamu, ndidzakutumizirani temberero, ndi kutemberera madalitso anu; inde, ndawatemberera kale chifukwa simuliika mumtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa