Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 8:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo Filipo anatsikira kumzinda wa ku Samariya, nawalalikira iwo Khristu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo Filipo anatsikira kumudzi wa ku Samariya, nawalalikira iwo Khristu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Filipo adatsikira ku mzinda wa ku Samariya, namalalikira anthu akumeneko za Khristu, Mpulumutsi wolonjezedwa uja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Filipo anapita ku mzinda wa ku Samariya ndipo analalikira za Khristu kumeneko.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 8:5
18 Mawu Ofanana  

Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ndi mu Yudeya monse, ndi mu Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.


Ndipo m'mawa mwake tinachoka, ndipo tinafika ku Kesareya, ndipo m'mene tinalowa m'nyumba ya Filipo mlaliki, mmodzi wa asanu ndi awiri aja, tinakhala naye.


Ndipo masiku onse, mu Kachisi ndi m'nyumba, sanaleke kuphunzitsa ndi kulalikira Khristu Yesu.


Ndipo mau amene anakonda unyinji wonse; ndipo anasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi chikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo, ndi Prokoro, ndi Nikanore ndi Timoni, ndi Parmenasi, ndi Nikolasi, ndiye wopinduka wa ku Antiokeya:


Ndipo Saulo analikuvomerezana nao pa imfa yake. Ndipo tsikulo kunayamba kuzunza kwakukulu pa Mpingo unali mu Yerusalemu; ndipo anabalalitsidwa onse m'maiko a Yudeya ndi Samariya, koma osati atumwi ai.


Koma mngelo wa Ambuye analankhula ndi Filipo, nanena, Nyamuka, nupite mbali ya kumwera, kutsata njira yotsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Gaza; ndiyo ya chipululu.


Ndipo Filipo anamthamangira, namva iye alikuwerenga Yesaya mneneri, ndipo anati, Kodi muzindikira chimene muwerenga?


Koma Filipo anapezedwa ku Azoto; ndipo popitapita analalikira Uthenga Wabwino m'midzi yonse, kufikira anadza iye ku Kesareya.


Ndipo makamuwo ndi mtima umodzi anasamalira zonenedwa ndi Filipo, pamene anamva, napenya zizindikiro zimene anazichita.


Ndipo pomwepo m'masunagoge analalikira Yesu, kuti Iye ndiye Mwana wa Mulungu.


koma ife tilalikira Khristu wopachikidwa, kwa Ayudatu chokhumudwitsa, ndi kwa amitundu chinthu chopusa;


Pakuti ndinatsimikiza mtima kuti ndisadziwe kanthu mwa inu, koma Yesu Khristu, ndi Iye wopachikidwa.


Pakuti palibe munthu akhoza kuika maziko ena, koma amene aikidwako, ndiwo Yesu Khristu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa