Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 27:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo pamene padatsimikizika kuti tipite m'ngalawa kunka ku Italiya, anapereka Paulo ndi andende ena kwa kenturiyo dzina lake Julio, wa gulu la Augusto.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo pamene padatsimikizika kuti tipite m'ngalawa kunka ku Italiya, anapereka Paulo ndi andende ena kwa kenturiyo dzina lake Julio, wa gulu la Augusto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Zitatsimikizika kuti tiyenera kupita ku Italiya pa chombo, adampereka Paulo pamodzi ndi akaidi ena kwa mtsogoleri wa asilikali, dzina lake Julio, wa gulu la asilikali lochedwa gulu la Augusto.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Zitatsimikizika kuti tiyenera kupita ku Italiya pa sitima ya pa madzi, anamupereka Paulo pamodzi ndi a mʼndende ena kwa msilikali wolamulira asilikali 100, dzina lake Yuliyo, amene anali wa gulu la asilikali lotchedwa, Gulu la Mfumu.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 27:1
29 Mawu Ofanana  

Koma inu, munandipangira ine choipa; koma Mulungu anachipangira chabwino, kuti kuchitike monga lero, kupulumutsa amoyo anthu ambiri.


Chiweruzo cha Yehova chikhazikika chikhazikikire, zolingirira za m'mtima mwake ku mibadwomibadwo.


Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani; chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa.


Muli zolingalira zambiri m'mtima mwa munthu; koma uphungu wa Yehova ndiwo udzaimika.


Nkokoma kuti munthu asenze goli ali wamng'ono.


ndi okhala padziko lapansi onse ayesedwa achabe; ndipo Iye achita mwa chifuniro chake m'khamu la kumwamba ndi mwa okhala padziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye, Muchitanji?


Ndipo anali naye akudikira Yesu, anaona chivomezi, ndi zinthu zimene zinachitidwa, anaopa kwambiri, nanena, Indedi Uyu ndiye Mwana wa Mulungu.


Ndipo pamene kenturiyo anaona chinachitikacho, analemekeza Mulungu, nanena, Zoonadi munthu uyu anali wolungama.


Ndipo kapolo wa kenturiyo, wokondedwa naye, anadwala, nafuna kutsirizika.


Ndipo kunali munthu ku Kesareya, dzina lake Kornelio, kenturiyo wa gulu lotchedwa la Italiya,


Ndipo anati, Kornelio kenturiyoyo, munthu wolungama ndi wakuopa Mulungu, amene mtundu wonse wa Ayuda umchitira umboni, anachenjezedwa ndi mngelo woyera kuti atumize nakuitaneni mumuke kunyumba yake, ndi kumvetsa mau anu.


Pamene anaona masomphenyawo, pomwepo tinayesa kutulukira kunka ku Masedoniya, poganizira kuti Mulungu anaitanira ife kulalikira Uthenga Wabwino kwa iwo.


Ndipo anapeza Myuda wina dzina lake Akwila, fuko lake la ku Ponto, atachoka chatsopano ku Italiya, pamodzi ndi mkazi wake Prisila, chifukwa Klaudio analamulira Ayuda onse achoke mu Roma; ndipo Paulo anadza kwa iwo:


Ndipo zitatha izi, Paulo anatsimikiza mu mzimu wake, atapita pa Masedoniya ndi Akaya, kunka ku Yerusalemu, kuti, Nditamuka komweko ndiyenera kuonanso ku Roma.


Ndipo posachedwa iye anatenga asilikali ndi akenturiyo, nathamanga, nawatsikira; ndipo iwowa, pakuona kapitao wamkulu ndi asilikali, analeka kumpanda Paulo.


Ndipo pakumva ichi kenturiyoyo, ananka kwa kapitao wamkulu, namuuza, nanena, Nchiyani ichi uti uchite? Pakuti munthuyo ndiye Mroma.


Ndipo usiku wake Ambuye anaimirira pa iye, nati, Limbika mtima; pakuti monga wandichitira umboni ku Yerusalemu, koteronso uyenera kundichitira umboni ku Roma.


Ndipo Paulo anadziitanira kenturiyo wina, nati, Pita naye mnyamata uyu kwa kapitao wamkulu; pakuti ali nako kanthu kakumfotokozera iye.


Ndipo analamulira kenturiyo amsunge iye, koma akhale nao ufulu, ndipo asaletse anthu ake kumtumikira.


Pamenepo Fesito, atakamba ndi aphungu ake, anayankha, Wanena, Nditulukira kwa Kaisara; kwa Kaisara udzapita.


Koma ndinapeza ine kuti sanachite kanthu koyenera imfa iye; ndipo popeza iye yekha anati akatulukire kwa Augusto, ndatsimikiza mtima kumtumizako.


Koma kenturiyo anakhulupirira watsigiro ndi mwini ngalawa makamaka, wosasamala mau a Paulo.


Koma kenturiyo, pofuna kupulumutsa Paulo, anawaletsa angachite cha uphungu wao; nalamula kuti iwo akukhoza kusambira ayambe kudziponya m'nyanja, nafike pamtunda,


Ndipo kenturiyo anapezako ngalawa ya ku Aleksandriya, ilikupita ku Italiya, ndipo anatilongamo.


Ndipo titapulumuka, pamenepo tinadziwa kuti chisumbucho chinatchedwa Melita.


Ndipo pamene tinalowa mu Roma, analola Paulo akhale pa yekha ndi msilikali womdikira iye.


Perekani moni kwa atsogoleri anu onse, ndi oyera mtima onse. Akupatsani moni iwo a ku Italiya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa