Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 26:5 - Buku Lopatulika

5 andidziwa ine chiyambire, ngati afuna kuchitapo umboni, kuti ndinakhala Mfarisi monga mwa mpatuko wolunjikitsitsa wa chipembedzero chathu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 andidziwa ine chiyambire, ngati afuna kuchitapo umboni, kuti ndinakhala Mfarisi monga mwa mpatuko wolunjikitsitsa wa chipembedzero chathu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Iwo adandidziŵa kuyambira kale, ndipo ngati afuna, angathe kundichitira umboni kuti moyo wanga wonse ndakhala Mfarisi, mmodzi wa gulu lija limene limasamala chipembedzo chathu koposa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Iwo akundidziwa kuyambira kalekale ndipo angathe kuchitira umboni kuti ndakhala ndili Mfarisi moyo wanga wonse, mmodzi wa gulu limene limasamala chipembedzo chathu koposa.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 26:5
7 Mawu Ofanana  

Koma anauka ena a mpatuko wa Afarisi okhulupirira, nati, Kuyenera kuwadula iwo, ndi kuwauza kuti asunge chilamulo cha Mose.


Ine ndine munthu Myuda, wobadwa mu Tariso wa Silisiya, koma ndaleredwa m'mzinda muno, pa mapazi a Gamaliele, wolangizidwa monga mwa chitsatidwe chenicheni cha chilamulo cha makolo athu, ndipo ndinali wachangu, cholinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero;


Monganso mkulu wa ansembe andichitira umboni, ndi bwalo lonse la akulu; kwa iwo amenenso ndinalandira makalata kunka nao kwa abale, ndipo ndinapita ku Damasiko, kuti ndikatenge iwonso akukhala kumeneko kudza nao omangidwa ku Yerusalemu, kuti alangidwe.


Koma pozindikira Paulo kuti ena ndi Asaduki, ndi ena Afarisi, anafuula m'bwalomo, Amuna, abale, ine ndine Mfarisi, mwana wa Afarisi: andinenera mlandu wa chiyembekezo ndi kuuka kwa akufa.


Koma ichi ndivomera kwa inu, kuti monga mwa Njira yonenedwa mpatuko, momwemo nditumikira Mulungu wa makolo athu, ndi kukhulupirira zonse zili monga mwa chilamulo, ndi zolembedwa mwa aneneri;


Pakuti tapeza munthuyu ali ngati mliri, ndi woutsa mapanduko kwa Ayuda onse m'dziko lonse lokhalamo anthu, ndi mtsogoleri wa mpanduko wa Anazarene;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa