Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 18:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo Ambuye anati kwa Paulo usiku m'masomphenya, Usaope, koma nena, usakhale chete;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo Ambuye anati kwa Paulo usiku m'masomphenya, Usaope, koma nena, usakhale chete;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Tsiku lina usiku Ambuye adaonekera Paulo m'masomphenya namuuza kuti, “Usaope, koma upitirire kulalika, osakhala chete ai,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Usiku wina Ambuye anaonekera kwa Paulo mʼmasomphenya namuwuza kuti, “Usaope, pitiriza kuyankhula, usakhale chete.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 18:9
17 Mawu Ofanana  

Fuula zolimba, usalekerere, kweza mau ako ngati lipenga, ndi kuwafotokozera anthu anga cholakwa chao, ndi banja la Yakobo machimo ao.


Koma iwe ukwinde m'chuuno mwako, nuuke, nunene kwa iwo zonse zimene ndikuuza iwe; usaope nkhope zao ndingakuopetse iwe pamaso pao.


Munayandikira tsiku la kukuitanani ine; munati, Usaope.


Nyamuka, pita ku Ninive mzinda waukulu uja, nuulalikire uthenga umene ndikuuza.


Koma ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu ya Yehova, ndi chiweruzo, ndi chamuna, kufotokozera Yakobo kulakwa kwake, ndi kwa Israele tchimo lake.


Ndipo masomphenya anaonekera kwa Paulo usiku: Panali munthu wa ku Masedoniya alinkuimirira, namdandaulira kuti, Muolokere ku Masedoniya kuno, mudzatithangate ife.


chifukwa Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo palibe munthu adzautsana ndi iwe kuti akuipse; chifukwa ndili nao anthu ambiri m'mzinda muno.


ndipo ndinamuona Iye, nanena nane, Fulumira, tuluka msanga mu Yerusalemu; popeza sadzalandira umboni wako wakunena za Ine.


Ndipo usiku wake Ambuye anaimirira pa iye, nati, Limbika mtima; pakuti monga wandichitira umboni ku Yerusalemu, koteronso uyenera kundichitira umboni ku Roma.


Koma ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lake Ananiya; ndipo Ambuye anati kwa iye m'masomphenya, Ananiya. Ndipo anati, Ndili pano, Ambuye,


Kodi sindine mfulu? Kodi sindine mtumwi? Kodi sindinaone Yesu Ambuye wathu? Kodi simuli inu ntchito yanga mwa Ambuye?


koma tingakhale tidamva zowawa kale, ndipo anatichitira chipongwe, monga mudziwa, ku Filipi, tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m'kutsutsana kwambiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa