Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 18:10 - Buku Lopatulika

10 chifukwa Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo palibe munthu adzautsana ndi iwe kuti akuipse; chifukwa ndili nao anthu ambiri m'mzinda muno.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 chifukwa Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo palibe munthu adzautsana ndi iwe kuti akuipse; chifukwa ndili nao anthu ambiri m'mudzi muno.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 pakuti Ine ndili nawe pamodzi. Palibe munthu adzakukhudza kuti akuchite choipa, ndipo ndili nawo anthu ambiri mumzinda muno.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Pakuti Ine ndili nawe, palibe aliyense amene adzakukhudza ndi kukuchitira choyipa, chifukwa mu mzinda muno ndili ndi anthu ambiri.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 18:10
26 Mawu Ofanana  

Ndipo tsopano muka, ndipo Ine ndidzakhala m'kamwa mwako, ndi kukuphunzitsa chomwe ukalankhule.


usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.


Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.


Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.


Panganani upo, koma udzakhala chabe; nenani mau, koma sadzachitika; pakuti Mulungu ali pamodzi ndi ife.


Onani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamutcha dzina lake, Imanuele. Ndilo losandulika, Mulungu nafe.


komatu inu, matsitsi onse a m'mutu mwanu awerengedwa.


ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.


Ndipo silidzaonongeka tsitsi limodzi la pamutu panu.


Ndipo nkhosa zina ndili nazo, zimene sizili za khola ili; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mau anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi.


ndipo si chifukwa cha mtunduwo wokha ai, koma kuti akasonkhanitse pamodzi ana a Mulungu akubalalikawo.


Simoni wabwereza kuti poyamba Mulungu anayang'anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake.


ati Ambuye, amene azidziwitsa zinthu zonsezo chiyambire dziko lapansi.


Ndipo anakhala komwe chaka chimodzi kudza miyezi isanu ndi umodzi; naphunzitsa mau a Mulungu mwa iwo.


Ndipo Ambuye anati kwa Paulo usiku m'masomphenya, Usaope, koma nena, usakhale chete;


Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?


Ndipo ananena kwa ine, Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa mu ufooko. Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m'mafooko anga, kuti mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.


Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konsekonse, ndi amitundu onse amve; ndipo ndinalanditsidwa m'kamwa mwa mkango.


Ambuye akhale ndi mzimu wako. Chisomo chikhale nanu.


Palibe munthu adzatha kuima pamaso pako masiku onse a moyo wako; monga ndinakhala ndi Mose momwemo ndidzakhala ndi iwe; sindidzakusowa, sindidzakusiya.


Kodi sindinakulamulire iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kulikonse umukako.


Ndipo pamene Yehova anawaukitsira oweruza, Yehova anakhala naye woweruzayo, nawapulumutsa m'dzanja la adani ao masiku onse a woweruzayo; pakuti Yehova anagwidwa chisoni pa kubuula kwao chifukwa cha iwo akuwapsinja ndi kuwatsendereza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa