Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 13:12 - Buku Lopatulika

12 Pamenepo kazembe, pakuona chochitikacho anakhulupirira, nadabwa nacho chiphunzitso cha Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Pamenepo kazembe, pakuona chochitikacho anakhulupirira, nadabwa nacho chiphunzitso cha Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Pamene bwanamkubwa uja adaona zimene zidachitikazo, adakhulupirira. Adaadabwa nazo zimene iwo adaaphunzitsa za Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Pamene mkulu wa bomayo anaona zimene zinachitika anakhulupirira pakuti anadabwa ndi chiphunzitso cha Ambuye.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 13:12
20 Mawu Ofanana  

Ndipo anali naye akudikira Yesu, anaona chivomezi, ndi zinthu zimene zinachitidwa, anaopa kwambiri, nanena, Indedi Uyu ndiye Mwana wa Mulungu.


Ndipo onse anamchitira Iye umboni nazizwa ndi mau a chisomo akutuluka m'kamwa mwake; nanena, Kodi uyu si mwana wa Yosefe?


Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkulu wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzacheza ndi anthu ake.


Anyamatawo anayankha, Nthawi yonse palibe munthu analankhula chotero.


Ndipo pakumva ichi amitundu anakondwera, nalemekeza mau a Mulungu; ndipo anakhulupirira onse amene anaikidwiratu kumoyo wosatha.


Ndipo mau a Ambuye anabukitsidwa m'dziko lonse.


ameneyo anali ndi kazembe Sergio Paulo, ndiye munthu wanzeru. Yemweyo anaitana Barnabasi ndi Saulo, nafunitsa kumva mau a Mulungu.


Koma Elimasi watsengayo (pakuti dzina lake litero posandulika) anawakaniza, nayesa kupatutsa kazembe asakhulupirire.


Koma Paulo ndi Barnabasi anakhalabe mu Antiokeya, nalinkuphunzitsa, ndi kulalikira mau a Ambuye pamodzi ndi ena ambiri.


Patapita masiku, Paulo anati kwa Barnabasi, Tibwerere, tizonde abale m'mizinda yonse m'mene tinalalikiramo mau a Ambuye, tione mkhalidwe wao.


Tsono pamene Galio anali chiwanga cha Akaya, Ayuda ndi mtima umodzi anamuukira Paulo, nanka naye kumpando wachiweruziro,


Ndipo anachita chomwecho zaka ziwiri; kotero kuti onse akukhala mu Asiya anamva mau a Ambuye, Ayuda ndi Agriki.


Chotero mau a Ambuye anachuluka mwamphamvu napambana.


Ngati tsono Demetrio ndi amisiri okhala naye, ali ndi mlandu ndi munthu, mabwalo a milandu alipo, ndi ziwanga zilipo; anenezane.


Onsewo anali ngati amuna khumi ndi awiri.


Koma pafupi pamenepo panali minda, mwini wake ndiye mkulu chisumbucho, dzina lake Publio; amene anatilandira ife, natichereza okoma masiku atatu.


Ndipo sanathe kuipambana nzeru ndi Mzimu amene analankhula naye.


Pamenepo iwo, atatha kuchita umboni ndi kulankhula mau a Ambuye, anabwera kunka ku Yerusalemu, nalalikira Uthenga Wabwino kumidzi yambiri ya Asamariya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa