Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 12:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo adapha ndi lupanga Yakobo mbale wa Yohane.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo adapha ndi lupanga Yakobo mbale wa Yohane.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Adalamula kuti Yakobe, mbale wake wa Yohane, aphedwe ndi lupanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Iye analamula kuti Yakobo mʼbale wa Yohane, aphedwe ndi lupanga.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 12:2
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Ahabu anauza Yezebele zonse anazichita Eliya, ndi m'mene anawaphera ndi lupanga aneneri onsewo.


Ndipo anati, Ine ndinachitira changu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israele anasiya chipangano chanu, napasula maguwa anu a nsembe, napha aneneri anu ndi lupanga, ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuuchotsa.


ndipo anamtulutsa Uriya mu Ejipito, nanka naye kwa Yehoyakimu mfumu; amene anamupha ndi lupanga, naponya mtembo wake m'manda a anthu achabe.


Iye ananena kwa iwo, Chikho changa mudzamweradi; koma kukhala kudzanja lamanja kwanga ndi kulamanzere, sikuli kwanga kupatsa, koma kuli kwa iwo omwe kwakonzedweratu ndi Atate wanga.


Ndipo anadza kwa Iye Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedeo, nanena naye, Mphunzitsi, tifuna kuti mudzatichitire chimene chilichonse tidzapempha kwa Inu.


Koma Yesu anati kwa iwo, Simudziwa chimene muchipempha. Mukhoza kodi kumwera chikho chimene ndimwera Ine? Kapena kubatizidwa ndi ubatizo umene ndibatizidwa nao Ine?


Ndipo anati kwa Iye, Tikhoza. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Chikho chimene ndimwera Ine mudzamwera; ndipo ubatizo umene ndibatizidwa nao Ine, mudzabatizidwa nao;


Koma nyengo imeneyo Herode mfumu anathira manja ena a mu Mpingo kuwachitira zoipa.


anaponyedwa miyala, anachekedwa pakati, anayesedwa, anaphedwa ndi lupanga, anayendayenda ovala zikopa zankhosa, ndi zikopa zambuzi, nakhala osowa, osautsidwa, ochitidwa zoipa,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa