Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 9:39 - Buku Lopatulika

39 ndipo onani, umamgwira iye mzimu, nafuula modzidzimuka; ndipo umamng'amba iye ndi kumchititsa thovu pakamwa, suchoka pa iye, koma umsautsa koopsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 ndipo onani, umamgwira iye mzimu, nafuula modzidzimuka; ndipo umamng'amba iye ndi kumchititsa thovu pakamwa, nuchoka pa iye mwa unyenzi, numgola iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 Ali ndi mzimu woipa umene umati ukamugwira, amayamba kukuwa mwadzidzidzi. Tsono ukamzunguza kolimba, mwanayu amangoti thovu tututu kukamwa. Ndipo sumusiya mpaka utampweteka ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 Chiwanda chikamugwira amafuwula mwadzidzidzi; chimamugwedeza kolimba mpaka kutuluka thovu kukamwa. Sichimusiya ndipo chikumuwononga.

Onani mutuwo Koperani




Luka 9:39
11 Mawu Ofanana  

ndipo ponse pamene umgwira, umgwetsa; ndipo achita thovu, nakukuta mano, nanyololoka; ndipo ndinalankhula nao ophunzira anu kuti autulutse; koma sanakhoze.


Ndipo anadza naye kwa Iye; ndipo pakumuona, pomwepo mzimuwo unamng'amba koopsa; ndipo anagwa pansi navimvinika ndi kuchita thovu.


Ndipo pamene unafuula, numng'ambitsa, unatuluka; ndipo mwana anakhala ngati wakufa; kotero kuti ambiri ananena, Wamwalira.


Ndipo Yesu anamdzudzula iye, nanena, Tonthola, nutuluke mwa iye. Ndipo chiwandacho m'mene chinamgwetsa iye pakati, chinatuluka mwa iye chosampweteka konse.


Pakuti Iye adalamula mzimu wonyansa utuluke mwa munthuyo. Pakuti nthawi zambiri unamgwira; ndipo anthu anammanga ndi maunyolo ndi matangadza kumsungira; ndipo anamwetula zomangirazo, nathawitsidwa ndi chiwandacho kumapululu.


Ndipo onani, anafuula munthu wa m'khamulo, nanena, nati, Mphunzitsi, ndikupemphani, yang'anirani mwana wanga; chifukwa ndiye mmodzi yekha wa ine:


Ndipo ndinapempha ophunzira anu kuti autulutse; koma sanathe.


Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m'choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.


Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:


Ndipo linali nayo Mfumu yakulilamulira, mngelo wa chiphompho chakuya; dzina lake mu Chihebri Abadoni, ndi mu Chigriki ali nalo dzina Apoliyoni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa