Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 9:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo anati kwa iwo, Koma inu munena kuti Ine ndine yani? Ndipo anayankha Petro, nati, Khristu wa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo anati kwa iwo, Koma inu munena kuti Ine ndine yani? Ndipo anayankha Petro, nati, Khristu wa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Nanga inuyo, mumati ndine yani?” Petro adayankha kuti, “Inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja wa Mulungu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Iye anafunsa kuti, “Koma nanga inu mumati Ine ndine yani?” Petro anayankha kuti, “Mpulumutsi wolonjezedwa uja wa Mulungu.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 9:20
20 Mawu Ofanana  

nati, Muganiza bwanji za Khristu? Ali mwana wa yani? Iwo ananena kwa Iye, Wa Davide.


Koma Yesu anangokhala chete. Ndipo mkulu wa ansembe ananena kwa Iye, Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiwe Khristu, Mwana wa Mulungu.


Ndipo ngati mupatsa moni abale anu okhaokha, muchitanji choposa ena? Kodi angakhale anthu akunja sachita chomwecho?


Koma anakhala chete, osayankha kanthu. Mkulu wa ansembe anamfunsanso, nanena naye, Kodi Iwe ndiwe Khristu, Mwana wake wa Wolemekezeka?


Ndipo Iye anawafunsa, Koma inu munena kuti ndine yani? Petro anayankha nanena naye, Ndinu Khristu.


nanena, Ngati uli Khristu, utiuze. Ndipo anati kwa iwo, Ndikakuuzani, simudzavomereza;


Ndipo anayankha nati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndi ena, kuti anauka mmodzi wa aneneri akale.


Anayamba iye kupeza mbale wake yekha Simoni, nanena naye, Tapeza ife Mesiya (ndiko kusandulika Khristu).


Natanaele anayankha Iye, Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu mfumu ya Israele.


Ananena ndi Iye, Inde Ambuye; ndakhulupirira ine kuti Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu, wakudza m'dziko lapansi.


koma zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Khristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupirira mukhale nao moyo m'dzina lake.


Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu zilizonse ndinazichita: ameneyu sali Khristu nanga?


ndipo ananena kwa mkazi, kuti, Tsopano sitikhulupirira chifukwa cha kulankhula kwako: pakuti tamva tokha, ndipo tidziwa kuti Mpulumutsi wa dziko lapansi ndi Iyeyu ndithu.


Ena ananena, Uyu ndi Khristu. Koma ena ananena, Kodi Khristu adza kutuluka mu Galileya?


natsimikiza, kuti kunayenera Khristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Khristu.


Ndipo monga anapita panjira pao, anadza kumadzi akuti; ndipo mdindoyo anati, Taonapo madzi; chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe?


Koma Saulo anakula makamaka mumphamvu, nadodometsa Ayuda akukhala mu Damasiko, nawatsimikizira kuti ameneyo ndi Khristu.


Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Khristu wabadwa kuchokera kwa Mulungu; ndipo yense wakukonda Iye amene anabala akondanso iye amene anabadwa wochokera mwa Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa