Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 7:37 - Buku Lopatulika

37 Ndipo onani, mkazi wochimwa, amene anali m'mzindamo; ndipo pakudziwa kuti Yesu analikuseama pachakudya m'nyumba ya Mfarisi, anatenga nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

37 Ndipo onani, mkazi wochimwa, amene anali m'mudzimo; ndipo pakudziwa kuti Yesu analikuseama pachakudya m'nyumba ya Mfarisi, anatenga nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

37 M'mudzimo mudaali mai wachiwerewere. Iyeyu atamva kuti Yesu akudya m'nyumba ya Mfarisi uja, adabwera ndi nsupa yagalasi ya mafuta onunkhira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

37 Mayi amene amakhala moyo wauchimo mu mzindawo atadziwa kuti Yesu akudya ku nyumba ya Mfarisiyo, anabweretsa botolo la mafuta onunkhira a alabasta.

Onani mutuwo Koperani




Luka 7:37
18 Mawu Ofanana  

Ndani wa awiriwo anachita chifuniro cha atate wake? Iwo ananena, Woyambayo. Yesu ananena kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti amisonkho ndi akazi achiwerewere amatsogolera inu, kulowa mu Ufumu wa Kumwamba.


Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafune kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa.


Ndipo m'mene anachiona anadandaula onse, nanena, Analowa amchereze munthu ali wochimwa.


Ndipo Afarisi ndi alembi ao anang'ung'udza kwa ophunzira ake, nanena, kuti, Bwanji inu mukudya ndi kumwa pamodzi ndi anthu amisonkho ndi ochimwa?


Sindinadza Ine kuitana olungama, koma ochimwa kuti atembenuke mtima.


Mwana wa Munthu wafika wakudya ndi wakumwa; ndipo munena, Onani, munthu wosusuka ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi anthu ochimwa!


Ndipo mmodzi wa Afarisi anamuitana Iye kuti akadye naye. Ndipo analowa m'nyumba ya Mfarisi, naseama pachakudya.


Koma ndiye Maria uja anadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira bwino, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake, amene mlongo wake Lazaro anadwala.


Pamenepo anamuitana kachiwiri munthuyo amene anali wosaona, nati kwa iye, Lemekeza Mulungu; tidziwa kuti munthuyo ali wochimwa.


Tidziwa kuti Mulungu samvera ochimwa. Koma ngati munthu aliyense akhala wopembedza Mulungu nachita chifuniro chake, amvera ameneyo.


Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Khristu adatifera ife.


Mauwa ali okhulupirika ndi oyenera konse kuti awalandire, kuti Khristu Yesu anadza kudziko lapansi kupulumutsa ochimwa; wa iwowa ine ndine woposa;


podziwa ichi, kuti lamulo siliikika kwa munthu wolungama, koma kwa osaweruzika ndi osamvera lamulo, osapembedza, ndi ochimwa, osalemekeza ndi amnyozo, akupha atate ndi akupha amai, akupha anzao,


Ndipo ngati munthu wolungama apulumuka ndi kuyesetsa kokhakokha, munthu wosapembedza ndi wochimwa adzaoneka kuti?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa