Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 6:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo kunali tsiku lina la Sabata, Iye analowa m'sunagoge, naphunzitsa. Ndipo munali munthu momwemo, ndipo dzanja lake lamanja linali lopuwala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo kunali tsiku lina la Sabata, Iye analowa m'sunagoge, naphunzitsa. Ndipo munali munthu momwemo, ndipo dzanja lake lamanja linali lopuwala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Pa tsiku lina la Sabata Yesu adaloŵa m'nyumba yamapemphero nkumaphunzitsa. M'menemo munali munthu wina wopuwala dzanja lamanja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 La Sabata lina Iye analowa mʼsunagoge kukaphunzitsa ndipo mʼmenemo anapeza munthu wadzanja lolumala.

Onani mutuwo Koperani




Luka 6:6
14 Mawu Ofanana  

Ndipo kunachitika, pakumva mfumu mau a munthu wa Mulungu amene anawafuula, kutemberera guwa la nsembe mu Betele, Yerobowamu anatansa dzanja lake ali ku guwalo, nati, Mgwireni iye. Ndipo dzanja lake analitansira kwa iye linauma, kuti sanathe kulifunyatitsanso.


Tsoka mbusa wopanda pake, wakusiya zoweta! Lupanga padzanja lake, ndi pa diso lake la kumanja; dzanja lake lidzauma konse, ndi diso lake lamanja lidzada bii.


Ndipo Yesu anayendayenda mu Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.


Ndipo analikuphunzitsa m'sunagoge mwina, tsiku la Sabata.


Ndipo Yesu anayankha nati kwa achilamulo ndi Afarisi, nanena, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchiritsa, kapena iai?


Ndipo anadza ku Nazarete, kumene analeredwa; ndipo tsiku la Sabata analowa m'sunagoge, monga anazolowera, naimiriramo kuwerenga m'kalata.


Ndipo Iye anatsika nadza ku Kapernao, ndiwo mzinda wa ku Galileya. Ndipo analikuwaphunzitsa iwo pa Sabata; ndipo anadabwa ndi chiphunzitso chake;


Ndipo kunali tsiku la Sabata, Iye analinkupita pakati pa minda ya tirigu; ndipo ophunzira ake analinkubudula ngala za tirigu, nazifikisa m'manja mwao, nadya.


Ndipo Iye ananena kwa iwo, kuti, Mwana wa Munthu ali Mbuye wa tsiku la Sabata.


M'menemo munagona khamu lalikulu la anthu odwala, akhungu, opunduka miyendo, opuwala.


Ena pamenepo mwa Afarisi ananena, Munthu uyu sachokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata. Koma ena ananena, Munthu ali wochimwa akhoza bwanji kuchita zizindikiro zotere? Ndipo panali kutsutsana mwa iwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa