Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 6:29 - Buku Lopatulika

29 Iye amene akupanda iwe pa tsaya limodzi umpatsenso linzake; ndi iye amene alanda chofunda chako, usamkanize malaya ako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Iye amene akupanda iwe pa tsaya limodzi umpatsenso linzake; ndi iye amene alanda chofunda chako, usamkanize malaya ako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Ngati munthu akumenya pa tsaya, uperekere linalonso. Ndipo munthu akakulanda mwinjiro wako, umlole atenge ndi mkanjo womwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Ngati wina akumenyani patsaya limodzi mupatseninso tsaya linalo. Ngati wina akulanda mwinjiro wako, umulole atenge ndi mkanjo omwe.

Onani mutuwo Koperani




Luka 6:29
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Mefiboseti anati kwa mfumu, Lingakhale lonselo alitenge, popeza mbuye wanga mfumu wabwera mumtendere kunyumba yake.


Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenana anayandikira, nampanda Mikaya patsaya, nati, Mzimu wa Yehova wandichokera bwanji kulankhula ndi iwe?


Ndinapereka msana wanga kwa omenya, ndi masaya anga kwa iwo amene anakudzula tsitsi langa; sindinabisire nkhope yanga manyazi ndi kulavulidwa.


Atembenuzire wompanda tsaya lake, adzazidwe ndi chitonzo.


Uzisonkhana tsopano magulumagulu, mwana wamkazi wa magulu iwe; watimangira misasa, adzapanda woweruza wa Israele ndi ndodo patsaya.


Pomwepo iwo anathira malovu pankhope pake, nambwanyula Iye; ndipo ena anampanda khofu,


Ndipo anamkulunga Iye m'maso, namfunsa, nati, Talota; anakupanda Iwe ndani?


Munthu aliyense akakupempha kanthu, umpatse; ndi iye amene alanda zako, usazipemphanso.


Koma m'mene Iye adanena izi, mmodzi wa anyamata akuimirirako anapanda Yesu khofu, ndi kuti, Kodi uyankha mkulu wa ansembe chomwecho?


Ndipo mkulu wa ansembe Ananiya analamulira akuimirirako ampande pakamwa pake.


Kufikira nthawi yomwe ino timva njala, timva ludzu, tili amaliseche, tikhomedwa, tilibe pokhazikika;


Koma pamenepo pali chosowa konsekonse mwa inu, kuti muli nayo milandu wina ndi mnzake. Chifukwa ninji simusankhula kulola kuipsidwa? Simusankhula chifukwa ninji kulola kunyengedwa?


Pakuti mulola ngati wina akuyesani inu akapolo, ngati wina alikwira inu, ngati wina alanda zanu, ngati wina adzikuza, ngati wina akupandani pankhope.


Pakuti munamva chifundo ndi iwo a m'ndende, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa chuma chanu, pozindikira kuti muli nacho nokha chuma choposa chachikhalire.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa