Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 6:26 - Buku Lopatulika

26 Tsoka inu, pamene anthu onse adzanenera inu zabwino! Pakuti makolo ao anawatero momwemo aneneri onama.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Tsoka inu, pamene anthu onse adzanenera inu zabwino! Pakuti makolo ao anawatero momwemo aneneri onama.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 “Ndinu atsoka, anthu onse akamakuyamikani. Paja makolo ao ankachitira aneneri onama akale zomwezi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Ndinu atsoka, anthu akamakuyamikirani, popeza makolo anu anawachitira aneneri onama zomwezi.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 6:26
18 Mawu Ofanana  

Siliva asungunuka m'mbiya, ndi golide m'ng'anjo, motero chomwe munthu achitama adziwika nacho.


amene amati kwa alauli, Mtima wanu usapenye; ndi kwa aneneri, Musanenere kwa ife zinthu zoona, munene kwa ife zinthu zamyadi, munenere zonyenga;


aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pakulamulira kwao; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzachita chiyani pomalizira pake?


Munthu akayenda ndi mtima wachinyengo ndi kunama, ndi kuti, Ndidzanenera kwa iwe za vinyo ndi chakumwa chakuledzeretsa; iye ndiye mneneri wa anthu ake.


Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m'kati mwao ali mimbulu yolusa.


Tsoka inu okhuta tsopano! Chifukwa mudzamva njala. Tsoka inu, akuseka tsopano! Chifukwa mudzachita maliro ndi kulira misozi.


Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu.


Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu; koma Ine lindida popeza Ine ndilichitira umboni, kuti ntchito zake zili zoipa.


Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Khristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa.


Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa