Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 5:2 - Buku Lopatulika

2 ndipo anaona ngalawa ziwiri zinakhala m'mbali mwa nyanja; koma asodzi a nsomba adatuluka m'menemo, nalikutsuka makoka ao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 ndipo anaona ngalawa ziwiri zinakhala m'mbali mwa nyanja; koma asodzi a nsomba adatuluka m'menemo, nalikutsuka makoka ao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Iye adaona zombo ziŵiri pamphepetepo. Asodzi anali atatulukamo, ndipo ankatsuka makoka ao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Iye anaona mabwato awiri ali mʼmphepete mwa nyanja, asodzi amene ankachapa makhoka awo atawasiya pamenepo.

Onani mutuwo Koperani




Luka 5:2
7 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene Yesu analikuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andrea, mbale wake, analikuponya khoka m'nyanja; popeza anali asodzi a nsomba.


Ndipo popitirirapo Iye anaona abale ena awiri, Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake, m'ngalawa, pamodzi ndi Zebedeo atate wao, analikusoka makoka ao; ndipo anaitana iwo.


Ndipo pakuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi Andrea, mbale wake wa Simoni, alinkuponya khoka m'nyanja; pakuti anali asodzi.


Ndipo atapita patsogolo pang'ono, anaona Yakobo, mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake, iwonso anali m'chombo nakonza makoka ao.


Ndipo panali, pakumkanikiza khamu la anthu, kudzamva mau a Mulungu, Iye analikuimirira m'mbali mwa nyanja ya Genesarete;


Ndipo Iye analowa m'ngalawa imodzi, ndiyo yake ya Simoni, nampempha iye akankhe pang'ono. Ndipo anakhala pansi m'menemo, naphunzitsa m'ngalawa makamuwo a anthu.


Andrea mbale wake wa Simoni Petro anali mmodzi wa awiriwo, anamva Yohane, namtsata Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa