Luka 5:19 - Buku Lopatulika19 Ndipo posapeza polowa naye, chifukwa cha unyinji wa anthu, anakwera pamwamba pa tsindwi, namtsitsira iye poboola pa tsindwi ndi kama wake, namfikitsa pakati pomwe pamaso pa Yesu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201419 Ndipo posapeza polowa naye, chifukwa cha unyinji wa anthu, anakwera pamwamba pa chindwi, namtsitsira iye poboola pa chindwi ndi kama wake, namfikitsa pakati pomwe pamaso pa Yesu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa19 Koma chifukwa anthu adaachuluka, sadapeze poloŵera naye. Motero adakwera pa denga, nachotsapo mapale ena, nkumutsitsa ndi machira ake omwe kumufikitsa pansi pakati pa anthu, pamaso pa Yesu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero19 Atalephera kupeza njira yochitira zimenezi chifukwa cha gulu la anthu, anakwera naye pa denga ali pa mphasa pomwepo ndi kumutsitsira mʼkati pakati pa gulu la anthu, patsogolo penipeni pa Yesu. Onani mutuwo |