Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 5:15 - Buku Lopatulika

15 Koma makamaka mbiri yake ya Iye inabuka: ndipo mipingo yambiri ya anthu inasonkhana kudzamvera, ndi kudzachiritsidwa nthenda zao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Koma makamaka mbiri yake ya Iye inabuka: ndipo mipingo yambiri ya anthu inasonkhana kudzamvera, ndi kudzachiritsidwa nthenda zao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Komabe mbiri ya Yesu inkawandirawandira, ndipo makamu ambiri a anthu ankasonkhana kuti amve mau ake, ndiponso kuti aŵachize nthenda zao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Koma mbiri yake inafalikirabe kwambiri kotero kuti magulu a anthu anabwera kudzamvetsera ndi kuti achiritsidwe ku matenda awo.

Onani mutuwo Koperani




Luka 5:15
13 Mawu Ofanana  

Kuopa Yehova ndiko mwambo wanzeru; ndipo chifatso chitsogolera ulemu.


Ndipo mbiri yake imene inabuka m'dziko lonse limenelo.


Koma iwo anatulukamo, nabukitsa mbiri yake m'dziko lonselo.


Ndipo mbiri yake inabuka pompaja kudziko lonse la Galileya lozungulirapo.


Koma iye anatuluka nayamba kulalikira ndithu, ndi kubukitsa mauwo, kotero kuti Yesu sanathe kulowanso poyera m'mudzi, koma anakhala padera m'mapululu; ndipo anadza kwa Iye anthu a kumalo onse.


Ndipo Yesu anachokako pamodzi ndi ophunzira ake nanka kunyanja: ndipo linamtsata khamu lalikulu la a ku Galileya, ndi a ku Yudeya,


Pomwepo pamene anthu a zikwizikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, Iye anayamba kunena kwa ophunzira ake poyamba, Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate cha Afarisi, chimene chili chinyengo.


Ndipo mipingo yambiri ya anthu inamuka naye; ndipo Iye anapotoloka, nati kwa iwo,


Ndipo khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye, chifukwa anaona zizindikiro zimene anachita pa odwala.


Momwemonso pali ntchito zokoma zinaonekera kale; ndipo zina zosati zotere sizingathe kubisika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa