Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 4:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo m'mene anamtsogolera anakwera naye, namuonetsa Iye maufumu onse a dziko lokhalamo anthu, m'kamphindi kakang'ono.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo m'mene anamtsogolera anakwera naye, namuonetsa Iye maufumu onse a dziko lokhalamo anthu, m'kamphindi kakang'ono.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Pambuyo pake Satana adatenga Yesu kupita naye pa malo okwera, ndipo pa kamphindi kakang'ono adamuwonetsa maiko a mafumu onse a pansi pano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Mdierekezi anamutengera Iye pamalo aatali ndipo mʼkamphindi namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani




Luka 4:5
11 Mawu Ofanana  

kuti kufuula kokondwera kwa woipa sikukhalira kutha, ndi chimwemwe cha wonyoza Mulungu chikhala kamphindi?


Ha? M'kamphindi ayesedwa bwinja; athedwa konse ndi zoopsa.


Ndipo Uthenga uwu Wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.


Pomwepo mdierekezi anamuka naye kuphiri lalitali, namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wao;


m'kamphindi, m'kuthwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osavunda, ndipo ife tidzasandulika.


ndi iwo akuchita nalo dziko lapansi, monga ngati osachititsa; pakuti maonekedwe a dziko ili apita.


Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero;


zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera;


Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa