Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 4:43 - Buku Lopatulika

43 Koma anati kwa iwo, Kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumizinda inanso: chifukwa ndinatumidwa kudzatero.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

43 Koma anati kwa iwo, Kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumidzi yinanso: chifukwa ndinatumidwa kudzatero.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

43 Koma Iye adaŵauza kuti, “Ndiyenera kukalalika Uthenga Wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu ku midzi inanso, pakuti ndizo zimene Mulungu adanditumira.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

43 Koma Iye anati, “Ine ndikuyenera kulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ku mizinda inanso chifukwa ichi ndi chimene ananditumira.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 4:43
12 Mawu Ofanana  

Idzani inu chifupi ndi Ine, imvani ichi; kuyambira pa chiyambi sindinanene m'tseri; chiyambire zimenezi, Ine ndilipo; ndipo tsopano Ambuye Mulungu wanditumiza Ine ndi mzimu wake.


Ndipo Yesu anayendayenda mu Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.


Ndipo m'mawa mwake anauka usikusiku, natuluka namuka kuchipululu, napemphera kumeneko.


Chifukwa chake Yesu anatinso kwa iwo, Mtendere ukhale ndi inu; monga Atate wandituma Ine, Inenso ndituma inu.


Tiyenera kugwira ntchito za Iye wondituma Ine, pokhala pali msana; ukudza usiku pamene palibe munthu angakhoze kugwira ntchito.


za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.


lalikira mau; chita nao pa nthawi yake, popanda nthawi yake; tsutsa, dzudzula, chenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa